Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limatanthauza Chiyani Likamanena Kuti “Mawu?”

Kodi Baibulo Limatanthauza Chiyani Likamanena Kuti “Mawu?”

Yankho la M’Baibulo

Nthawi zambiri mawu akuti “mawu a Mulungu” amatanthauza uthenga umodzi kapenanso mauthenga angapo ochokera kwa Mulungu. (Luka 11:28) M’mavesi ena m’Baibulo, mawu akuti “Mawu a Mulungu” kapena akuti “Mawu,” amagwiritsidwa ntchito ngati dzina la udindo.​—Chivumbulutso 19:13; Yohane 1:14.

Uthenga wochokera kwa Mulungu. Nthawi zambiri aneneri ankafotokoza kuti uthenga umene ankauza anthu unali mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, pamene Yeremiya ankafotokoza zokhudza zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo anayamba ndi mawu akuti, ‘Mawu a Yehova anadza kwa ine.’ (Yeremiya 1:4, 11, 13; 2:1 Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Komanso mneneri Samueli asanauze Sauli kuti Mulungu wamusankha kuti akhale mfumu, mneneriyo ananena kuti: “Ima kaye kuti ndikuuze mawu a Mulungu.”—1 Samueli 9:27.

Dzina la udindo. Dzina lakuti “Mawu,” ndi dzina la udindo la Yesu Khristu ndipo limagwiritsidwa ntchito m’Baibulo pofotokoza za Yesu ali kumwamba komanso padziko lapansi. Tiyeni tione chifukwa chake tikutero.

  • Mawu ameneyu anakhalapo zinthu zina zonse zisanalengedwe. Baibulo limanena kuti: “Pa chiyambi, panali wina wotchedwa Mawu . . . Ameneyu anali ndi Mulungu pa chiyambi.” (Yohane 1:1, 2) Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse . . . iye ali patsogolo pa zinthu zina zonse.”​—Akolose 1:13-15, 17.

  • Mawuyo anabwera padziko lapansi n’kudzakhala ngati munthu. Baibulo limati: “Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama ndi kukhala pakati pathu.” (Yohane 1:14) Khristu Yesu “anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo, ndi kukhala wofanana ndi anthu.”​—Afilipi 2:5-7.

  • Mawu ameneyu ndi Mwana wa Mulungu. Mtumwi Yohane atangomaliza kunena mawu ali pamwambawa akuti, “Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama,” ananenanso kuti: “Tinaona ulemerero wake, ulemerero wa mwana wobadwa yekha kwa bambo ake.” (Yohane 1:14) Mtumwiyu, analembanso kuti: “Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.”​—1 Yohane 4:15.

  • Mawu ali ngati Mulungu. Baibulo limanena kuti “Mawuyo anali mulungu.” Ponenanso zimenezi, Baibulo lina limati Mawu “anali waumulungu.” (Yohane 1:1; An American Translation) Yesu ndi “chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo.”—Aheberi 1:2, 3.

  • Mawu akulamulira monga mfumu. Baibulo limanena kuti pamutu pa Mawu a Mulungu, pali “zisoti zachifumu zambiri.” (Chivumbulutso 19:12, 13) Mawu amadziwikanso kuti, “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.” (Chivumbulutso 19:16) Yesu amatchedwa “Mfumu ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye wa olamulira monga ambuye.”​—1 Timoteyo 6:14, 15.

  • Mawu ali ndi udindo wolankhula m’malo mwa Mulungu. Ndipo dzina lakuti “Mawu,” limatithandiza kudziwa kuti Mulungu amagwiritsa ntchito Yesu kupereka uthenga ndiponso malangizo. Yesu anasonyeza kuti anali ndi udindo umenewu pamene ananena kuti: “Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula. . . . Choncho zimene ndimalankhula, monga mmene Atate anandiuzira, ndimazilankhula momwemo.”​—Yohane 12:49, 50.