Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Ali ndi Malo Enieni Amene Amakhala?

Kodi Mulungu Ali ndi Malo Enieni Amene Amakhala?

Yankho la m’Baibulo

 Inde. Mulungu ali ndi malo enieni amene amakhala ndipo ndi kumwamba. Taonani mavesi a m’Baibulo otsatirawa:

 Popemphera, Mfumu Solomo anati: “Inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika.”—1 Mafumu 8:43.

 Yesu Khristu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kwa ‘Atate wawo wakumwamba.’—Mateyu 6:9.

 Yesu ataukitsidwa, “analowa kumwamba kwenikweniko. Tsopano ali kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu.”—Aheberi 9:24.

 Mavesiwa akusonyeza kuti Yehova Mulungu ndi munthu weniweni ndipo sakhala paliponse koma amakhala kumwamba.