Pitani ku nkhani yake

Kodi Nkhani za M’Baibulo Ndi Maganizo a Mulungu?

Kodi Nkhani za M’Baibulo Ndi Maganizo a Mulungu?

Yankho la m’Baibulo

 Anthu ambiri amene analemba Baibulo amanena kuti Mulungu ndi amene anawauza zimene analembazo. Taonani zitsanzo izi:

  •  Mfumu Davide inati: “Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa, ndipo mawu ake anali palilime langa.”—2 Samueli 23:1, 2.

  •  Mneneri Yesaya anati: “[Izi ndi zimene] Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.”—Yesaya 22:15.

  • Mtumwi Yohane anati: “Chivumbulutso choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa.”—Chivumbulutso 1:1.