Pitani ku nkhani yake

Kodi Likasa la Pangano N’chiyani?

Kodi Likasa la Pangano N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Likasa la pangano linali bokosi lopatulika lomwe linapangidwa ndi Aisiraeli akale. Anapanga bokosili potsatira malangizo omwe Mulungu anawapatsa. M’bokosili ndi mmene ankaikamo “Umboni” kapena kuti Malamulo Khumi omwe analembedwa pamiyala iwiri.​—Ekisodo 25:8-10, 16; 31:18.

  • Linapangidwa bwanji? Kukula kwa Likasa limeneli kunali mikono iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi ndiponso mkono umodzi ndi hafu kutalika kuchoka pamwamba mpaka pansi. (Masentimita 111 m’litali, masentimita 67 m’lifupi ndiponso masentimita 67 kuchoka pamwamba mpaka pansi.) Bokosili linapangidwa ndi mtengo wa mthethe ndipo linapakidwa golide mkati ndi kunja komwe komanso linajambulidwa tinthu tokongoletsa. Chivindikiriro chake chinali chopangidwa ndi golide ndipo pamwamba pake cham’mbali, panali akerubi awiri agolide. Anaika akerubiwa moyang’anizana komanso atayang’ana pansi. Mapiko awo anali otambasulira m’mwamba ndipo ankaphimba chivindikiriro chija. Panalinso mphete 4 zopangidwa ndi golide zomwe zinali chapamwamba pa miyendo ya Likasalo. Anapanganso ndodo za mitengo ya mthethe yopaka golide n’kuilowetsa mu mphete zija kuti azinyamulira likasalo.​—Ekisodo 25:10-21; 37:6-9.

  • Linkasungidwa kuti? Poyamba linkasungidwa m’Chipinda Chopatulika ku chihema. Chihemachi chinali malo olambirira omwe ankatha kuwasamutsa ndipo nachonso chinapangidwa pa nthawi imene Likasa lija linapangidwa. Chipinda Chopatulika chinali chotchinga moti ansembe ndi anthu ena sankatha kuona mkati mwake. (Ekisodo 40:3, 21) Mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankatha kulowa m’chipindachi ndipo ankalowamo kamodzi pachaka, pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. (Levitiko 16:2; Aheberi 9:7) Kenako patapita nthawi, Solomo atamaliza kumanga kachisi, Likasa lija anakaliika m’Malo Oyera Koposa a m’kachisiyo.​—1 Mafumu 6:14, 19.

  • Cholinga chake chinali chiyani? Likasali linkagwiritsidwa ntchito kusungiramo zinthu zopatulika zomwe zinkakumbutsa Aisiraeli za pangano lomwe anapangana ndi Mulungu ku phiri la Sinai. Linalinso lofunika kwambiri pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.​—Levitiko 16:3, 13-17.

  • Ankaikamo chiyani? Miyala iwiri yomwe panalembedwa Malamulo Khumi, inali yoyamba kuikidwa m’Likasa. (Ekisodo 40:20) Kenako munaikidwanso mtsuko wagolide wokhala ndi mana komanso “ndodo ya Aroni imene inaphuka ija.” (Aheberi 9:4; Ekisodo 16:33, 34; Numeri 17:10) Zikuoneka kuti nthawi ina yake, mtsuko uja komanso ndodo ya Aroni, zinachotsedwamo mu Likasa lija chifukwa pamene Likasali linkakaikidwa mu Kachisi, zinthuzi munalibemo.​—1 Mafumu 8:9.

  • Ankayenda nalo bwanji? Likasa linkafunika kunyamulidwa pamapewa ndi Alevi pogwiritsa ntchito ndodo za mitengo ya mthethe zimene analowetsa m’mbali mwake. (Numeri 7:9; 1 Mbiri 15:15) Ndodozi zinkakhala m’mbali mwa Likasali nthawi zonse n’cholinga choti Alevi asayerekeze kuligwira. (Ekisodo 25:12-16) “Nsalu yotchinga” yomwe inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa, inkagwiritsidwa ntchito kuphimbira Likasa likamasamutsidwa.​—Numeri 4:5, 6. *

  • Linkaimira chiyani? Likasa linkaimira kuti Mulungu ali pamalopo. Mwachitsanzo, mtambo womwe unkakhala pamwamba pa Likasa m’Malo Oyera Koposa komanso womwe unkatsogolera Aisiraeli paulendo wawo, unkaimira kuti Yehova anali pakati pawo ndipo akuwadalitsa. (Levitiko 16:2; Numeri 10:33-36) Baibulo limanenanso kuti Yehova ‘ankakhala pa akerubi,’ kutanthauza akerubi omwe anaikidwa pachivindikiro cha Likasa. (1 Samueli 4:4; Salimo 80:1) Choncho akerubiwa anali “chifaniziro cha galeta” la Yehova. (1 Mbiri 28:18) Chifukwa choti Mfumu Davide ankadziwa zimene Likasa linkaimira, pa nthawi imene Likasa lija linasamutsidwira ku Ziyoni, iye analemba kuti Yehova “akukhala m’Ziyoni.”​—Salimo 9:11.

  • Mayina ena a Likasa. Baibulo limagwiritsa ntchito mayina angapo ponena za bokosi lopatulika limeneli. Limagwiritsa ntchito mayina ngati: “Likasa la umboni,” “Likasa la pangano,” “Likasa la Yehova” komanso “Likasa limene [Yehova] mumasonyezera mphamvu zanu.”​—Numeri 7:89; Yoswa 3:6, 13; 2 Mbiri 6:41.

    Chivindikiro cha Likasa, chinkadziwikanso kuti “chivundikiro chophimba machimo.” (1 Mbiri 28:11) Dzinali likusonyeza ntchito imene chivindikirocho chinkagwira pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Pa tsikuli, mkulu wa ansembe ankatenga magazi a nyama zimene zaperekedwa nsembe, n’kuwadontheza patsogolo pa chivindikirocho. Zimene mkulu wa ansembeyo ankachita, zinkathandiza kuti “aziphimba machimo ake, a nyumba yake ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.”​—Levitiko 16:14-17.

Kodi likasa la pangano lilipobe masiku ano?

Palibe umboni wotsimikiza kuti Likasali lilipobe. Komanso, Baibulo limasonyeza kuti Likasa si lofunikanso masiku ano chifukwa pangano lomwe linkagwira ntchito m’nthawi ya Aisiraeli, linalowedwa m’malo ndi “pangano latsopano.” Pangano latsopanoli linayamba kugwira ntchito chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Yeremiya 31:31-33; Aheberi 8:13; 12:24) N’chifukwa chake Baibulo linaneneratu kuti likasa la pangano silidzafunikanso ndipo anthu a Mulungu sadzalifunanso.​—Yeremiya 3:16.

Pangano latsopano litakhazikitsidwa, mtumwi Yohane anaona masomphenya. M’masomphenyawo anaona likasa la pangano lili kumwamba. (Chivumbulutso 11:15, 19) Likasa la pangano lomwe linaoneka kumwamba linkaimira kuti Yehova ali kumwambako komanso kuti anadalitsa pangano latsopanolo.

Kodi likasa la pangano linkagwiranso ntchito ngati chithumwa?

Ayi. Kukhala ndi likasa la pangano sikunkachititsa Aisiraeli kuti zinthu ziwayendere bwino. Mwachitsanzo, Aisiraeli anagonja pomenyana ndi anthu a mumzinda wa Ai ngakhale kuti pa nthawiyo anali ndi likasa la pangano kumsasa wawo. Aisiraeliwo anagonjetsedwa chifukwa cha kusakhulupirika kwa Akani. (Yoswa 7:1-6) Patapitanso nthawi, Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Afilisiti ngakhale kuti anapita ku nkhondoko ndi likasa la pangano. Pa nthawiyi anagonjetsedwa chifukwa cha makhalidwe oipa a Hofeni ndi Pinihasi omwe anali ansembe. (1 Samueli 2:12; 4:1-11) Pa nkhondoyo, Afilisiti analanda Likasa lija ndipo Yehova anawakantha ndi miliri mpaka pamene anakalibweza ku Isiraeli.​—1 Samueli 5:11–6:5.

Mbiri ya likasa la pangano

Chaka

Zimene Zinachitika

1513 B.C.E.

Bezaleli ndi anzake anapanga Likasa pogwiritsa ntchito zipangizo zomwe Aisiraeli anapereka.​—Ekisodo 25:1, 2; 37:1.

1512 B.C.E.

Mose anatsegulira Likasa, chihema komanso ntchito za unsembe.​—Ekisodo 40:1-3, 9, 20, 21.

1512 B.C.E.​ mpaka chitadutsa chaka cha 1070 B.C.E.

Likasa analisamutsira ku malo osiyanasiyana.​—Yoswa 18:1; Oweruza 20:26, 27; 1 Samueli 1:24; 3:3; 6:11-14; 7:1, 2.

Chitadutsa chaka cha 1070 B.C.E.

Mfumu Davide anapita nalo ku Yerusalemu.​—2 Samueli 6:12.

1026 B.C.E.

Likasa linakaikidwa mu kachisi wa Solomo ku Yerusalemu.​—1 Mafumu 8:1, 6.

642 B.C.E.

Mfumu Yosiya anakabwezera Likasa ku kachisi.​—2 Mbiri 35:3. *

Chisanafike chaka cha 607 B.C.E.

Zikuoneka kuti Likasali linachotsedwa m’kachisi. Komabe mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E., likasali silinalembedwe pa mndandanda wa zinthu zomwe zinapita ku Babulo. Silinalembedwenso pa mndandanda wa zinthu zomwe zinadzabwerera ku Yerusalemu.​—2 Mafumu 25:13-17; Ezara 1:7-11.

63 B.C.E.

Pompeyi yemwe anali mkulu wa asilikali achiroma, analengeza za kusowa kwa likasali atalifufuza m’Malo Oyera Koposa pamene anagonjetsa mzinda wa Yerusalemu. *

^ ndime 8 Aisiraeli akapanda kumvera lamulo la Yehova pa nkhani yosamutsa komanso kuphimba Likasa ndi nsalu yotchinga, ankakumana ndi mavuto oopsa.​—1 Samueli 6:19; 2 Samueli 6:2-7.​—1 Samuel 6:​19; 2 Samuel 6:​2-7.

^ ndime 31 Baibulo silifotokoza kuti ndi ndani anachotsa likasalo m’kachisi, kuti analichotsamo liti komanso chifukwa chomwe analichotsera.

^ ndime 35 Onani ndime 9 m’buku lakuti, The Histories, Book V lomwe analemba Tacitus.