Pitani ku nkhani yake

Kodi Pali Munthu Amene Anaonapo Mulungu?

Kodi Pali Munthu Amene Anaonapo Mulungu?

Yankho la m’Baibulo

 Palibe munthu amene anaonapo Mulungu. (Ekisodo 33:20; Yohane 1:18; 1 Yohane 4:12) Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye Mzimu,” ndipo munthu sangathe kuona thupi lauzimu limeneli.​—Yohane 4:24; 1 Timoteyo 1:17.

 Angelo amaona Mulungu bwinobwino chifukwa chakuti nawonso ali ndi matupi auzimu. (Mateyu 18:10) Komanso anthu ena akamwalira, amaukitsidwa ndi matupi auzimu n’kupita kumwamba. Choncho zimakhala zotheka kuti aone Mulungu.​—Afilipi 3:20, 21; 1 Yohane 3:2.

Kodi mungatani kuti “muone” Mulungu masiku ano?

 M’Baibulo, nthawi zambiri mawu akuti “kuona” amatanthauza kumvetsa zinthu. (Yesaya 6:10; Yeremiya 5:21; Yohane 9:39-41) Choncho, munthu akhoza kuona Mulungu masiku ano ndi ‘maso a mtima wake.’ Izi zingatheke ngati munthuyo ali ndi chikhulupiriro chimene chingamuthandize kudziwa bwino Mulungu. (Aefeso 1:18) Baibulo limafotokoza kuti tiyenera kuchita zinthu zotsatirazi kuti tikhale ndi chikhulupiriro choterocho:

  •   Tingaphunzire za makhalidwe a Mulungu monga chikondi, kuwolowa manja, nzeru ndiponso mphamvu zake, kudzera m’zinthu zimene iye analenga. (Aroma 1:20) Munthu wokhulupirika Yobu, ananena zoti waona Mulungu, atakumbutsidwa zinthu zimene Mulunguyo analenga.​—Yobu 42:5.

  •   Tingamudziwe Mulungu tikamaphunzira Baibulo. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Ukam’funafuna [Mulungu], adzalola kuti um’peze.”​—1 Mbiri 28:9; Salimo 119:2; Yohane 17:3.

  •   Tingaphunzire za Mulungu kudzera mwa Yesu. Izi zili choncho chifukwa chakuti Yesu anasonyeza bwino makhalidwe a Atate wake, Yehova Mulungu. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.”​—Yohane 14:9.

  •   Tizichita zinthu zosangalatsa Mulungu ndipo tiziona zimene akutichitira. Yesu anati: “Odala ndi anthu oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.” Monga mmene tafotokozera, ena amene amachita zinthu zosangalatsa Mulungu, akamwalira amaukitsidwa n’kupita kumwamba ndipo ‘amakaona Mulungu.’​—Mateyu 5:8; Salimo 11:7.

Kodi Mose, Abulahamu ndi anthu ena anaonadi Mulungu?

 Nkhani zina za m’Baibulo zimasonyeza ngati kuti anthu ena anaonadi Mulungu. Koma kumvetsa bwino nkhanizi kumasonyeza kuti anthuwo ankaona angelo kapena masomphenya okhudza Mulungu.

 Angelo.

Kale Mulungu ankatumiza angelo kwa anthu kuti akalankhule m’malo mwa iye. (Salimo 103:20) Mwachitsanzo, Mulungu analankhula ndi Mose pachitsamba choyaka moto. Baibulo limafotokoza kuti “Mose anaphimba nkhope yake, chifukwa anaopa kuyang’ana Mulungu woona.” (Ekisodo 3:4, 6) Koma sikuti Mose anaonadi Mulungu, chifukwa nkhaniyi imasonyeza kuti iye anaona “mngelo wa Yehova.”​—Ekisodo 3:2.

 Ndipotu Baibulo likamanena kuti Mulungu “anali kulankhula ndi Mose pamasom’pamaso,” limatanthauza kuti ankalankhula naye mwachikondi monga bwenzi lake. (Ekisodo 4:10, 11; 33:11) Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anapereka uthenga wake kwa Mose “kudzera mwa angelo,” choncho Moseyo sanaone nkhope ya Mulungu. (Agalatiya 3:19; Machitidwe 7:53) Komabe Mose anali ndi chikhulupiriro champhamvu moti Baibulo limasonyeza zoti ankachita zinthu “ngati kuti akuona Wosaonekayo.”​—Aheberi 11:27.

 Mofanana ndi mmene ankalankhulira Mose, Mulungu ankalankhulanso ndi Abulahamu kudzera mwa angelo. Munthu amene akuwerenga Baibulo ngati nyuzipepala, angaganize kuti Abulahamu ankalankhuladi ndi Mulungu. (Genesis 18:1, 33) Komabe nkhani ya Abulahamu imasonyeza kuti “amuna atatu” amene anabwera kunyumba kwake anali angelo amene anatumidwa ndi Mulungu, ndipo Abulahamuyo ankadziwa zimenezi. Choncho ankalankhula nawo ngati kuti akulankhula ndi Yehova mwachindunji.​—Genesis 18:2, 3, 22, 32; 19:1.

 Masomphenya.

Mulungu ankaonekera kwa anthu kudzera m’masomphenya, kapena kuti zinthu zimene anthuwo ankaona m’maganizo mwawo. Mwachitsanzo, Baibulo likamanena kuti Mose ndi Aisiraeli “anaona Mulungu wa Isiraeli,” limatanthauza kuti “iwo anaona masomphenya a Mulungu woona.” (Ekisodo 24:9-11) Mofanana ndi zimenezi nthawi zina Baibulo limanena kuti aneneri ‘ankaona Yehova.’ (Yesaya 6:1; Danieli 7:9; Amosi 9:1) Nkhani zonsezi zikusonyezeratu kuti anthuwo sankaona Mulungu weniweni koma ankangoona masomphenya.​—Yesaya 1:1; Danieli 7:2; Amosi 1:1.