Pitani ku nkhani yake

Kodi M’poyenera Kuti Akhristu Azigwiritsa Ntchito Njira Zakulera?

Kodi M’poyenera Kuti Akhristu Azigwiritsa Ntchito Njira Zakulera?

Yankho la m’Baibulo

Yesu sanalamule anthu amene amamutsatira kuti azibereka ana kapena ayi. Ndipo palibe mtumwi wa Yesu ngakhale m’modzi amene analamula anthu kuti azibereka ana kapena asamabereke. Komanso m’Baibulo mulibe vesi ngakhale limodzi limene limaletsa anthu kugwiritsira ntchito njira zakulera. Koma mfundo yomwe imagwira ntchito pa nkhani imeneyi ndi ya pa lemba la Aroma 14:12. Lembali limati: “Chotero aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.”

Choncho, mwamuna ndi mkazi wake ali ndi ufulu wosankha ngati akufuna kukhala ndi ana kapena ayi. Ngati iwo asankha kuti akhale ndi ana, angasankhenso okha kuti akhale ndi ana angati komanso nthawi imene akufuna kukhala ndi anawo. Ngati mwamuna ndi mkazi wake asankha kugwiritsa ntchito njira zakulera zomwe sizingachititse kuti achotse mimba, umenewo ndi ufulu komanso udindo wawo. Palibe munthu amene ayenera kuwauza zochita pa nkhaniyi.—Aroma 14:4, 10-13.