Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yochotsa Mimba?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yochotsa Mimba?

Yankho la m’Baibulo

Mulungu amaona kuti moyo, ngakhale wa mwana wosabadwa, ndi wopatulika. Ponena za Mulungu, Mfumu Davide anauziridwa kulemba kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” (Salimo 139:16) Mulungu ananena kuti munthu angaimbidwe mlandu ngati atavulaza mwana wosabadwa. Iye amaona kuti kupha mwana wosabadwa n’chimodzimodzi ndi kupha munthu.—Ekisodo 20:13; 21:22, 23.

Bwanji ngati pa nthawi imene mwana akubadwa papezeka mavuto ena ndipo banjalo likufunika kusankha pakati pa kupulumutsa moyo wa mwanayo kapena kupulumutsa moyo wa mayi ake? Pa nthawi ngati imeneyi banjalo lingasankhe lokha kuti lipulumutse moyo wa ndani.