Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ziwanda Zilipodi?

Kodi Ziwanda Zilipodi?

Yankho la m’Baibulo

Inde zilipodi. Ziwanda ndi “angelo amene anachimwa,” ndipo anaukira Mulungu. (2 Petulo 2:4) Mngelo woyambirira amene anakhala chiwanda ndi Satana Mdyerekezi ndipo Baibulo limamutchula kuti “wolamulira ziwanda.”—Mateyu 12:24, 26.

Angelo amene sanamvere m’nthawi ya Nowa

Baibulo limanena za angelo amene sanamvere Mulungu Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike. Limanena kuti: “Ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.” (Genesis 6:2) Angelo oipawo “anasiya malo awo okhala” kumwamba n’kuvala matupi aumunthu n’cholinga choti achite chiwerewere ndi akazi.—Yuda 6.

Chigumula chitayamba, angelo oipawo anavula matupi aumunthu aja n’kuthawira kumwamba. Komabe Mulungu sanawalole kuti akhalenso m’gulu la angelo ake. Zitatero angelowa sanathenso kuvala matupi a anthu ndipo chimenechi chinali chilango chawo.—Aefeso 6:11, 12.

 

Onaninso

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu

Baibulo limanena za angelo ndi ziwanda. Koma kodi n’zoona kuti kuli angelo komanso ziwanda? Kodi zochita zawo zingakhudze moyo wanu?