Pitani ku nkhani yake

Kodi Yesu Ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

Kodi Yesu Ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

Yankho la m’Baibulo

Anthu amene ankatsutsa Yesu anamunamizira kuti iye ananena zoti ndi wofanana ndi Mulungu. (Yohane 5:18; 10:30-33) Komabe, Yesu sananene kuti iye anali wofanana ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Iye anati: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28.

Anthu oyambirira amene ankatsatira Yesu sankamuona kuti anali wofanana ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti Yesu ataukitsidwa, Mulungu “anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.” Apa zikuonekeratu kuti Paulo sankakhulupirira zoti Yesu anali Mulungu Wamphamvuyonse. Zikanakhala kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse, kodi zikanatheka bwanji kuti akwezedwe n’kukhala pamalo apamwamba?—Afilipi 2:9.