Pitani ku nkhani yake

Kodi Yesu Anabadwa Liti?

Kodi Yesu Anabadwa Liti?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo silimanena deti lenileni limene Yesu Khristu anabadwa. Mabuku otsatirawa akusonyezanso kuti detili silidziwika.

  • “Deti lolondola limene Khristu anabadwa silidziwika.”​—New Catholic Encyclopedia.

  • “Deti lenileni limene Khristu anabadwa silidziwika.”​—Encyclopedia of Early Christianity.

Ngakhale kuti Baibulo silinena mwachindunji deti limene Yesu anabadwa, limafotokoza zinthu ziwiri zimene zinachitika m’nthawi imene anabadwa. Zinthu zimenezi zimapangitsa anthu ambiri kuvomereza kuti Yesu sanabadwe pa December 25.

Sanabadwe m’nyengo yozizira

  1. Kalembera. Patangotsala nthawi yochepa kuti Yesu abadwe, Kaisara Augusto anapereka lamulo lakuti “anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula.” Aliyense anayenera kukalembetsa “kumzinda wakwawo,” ndipo anthu ena anafunika kuyenda mlungu umodzi kapena kuposerapo kuti akafike kumzinda wakwawo. (Luka 2:​1-3) Mwina ankafuna kuti anthu akalembetse m’kaundula kuti adziwe anthu oyenera kupereka msonkho komanso kulembedwa usilikali, ndipo anthu sankasangalala ndi kalembera wotereyu. Choncho, n’zosakayikitsa kuti Augusto akanaputa anthu omwe ankawalamulira powakakamiza kuti apite kumidzi ya kwawo m’nyengo yozizira n’cholinga choti akalembetse.

  2. Nkhosa. Abusa “anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse mosinthana maulonda.” (Luka 2:8) Buku lina limanena kuti nkhosa zinkagona panja kuyambira kutatsala “mlungu umodzi kuti pasika achitike [kumapeto kwa March]” mpakana pakati pa mwezi wa November. Linanenanso kuti: “Zinkakhala m’khola nthawi yozizira ikayamba. Zimenezi zikusonyeza kuti deti la 25 December limene anthu amachita Khirisimasi si limene Yesu anabadwa chifukwa nthawiyi imakhala yozizira komanso Uthenga Wabwino umanena kuti abusa anali kugonera kubusa kuyang’anira nkhosa.”​—Daily Life in the Time of Jesus.

M’nyengo ya chilimwe

Tikhoza kupeza nthawi yoyerekezera imene Yesu anabadwa powerengera kuyambira nthawi imene anamwalira pa Pasika, Nisani 14 m’chaka cha 33 C.E., n’kumabwerera m’mbuyo. (Yohane 19:​14-16) Yesu anayamba utumiki wake ali ndi zaka 30 ndipo anauchita kwa zaka zitatu ndi hafu, choncho ayenera kuti anabadwa cha kumayambiriro kwa chaka cha 2 B.C.E.​—Luka 3:23.

N’chifukwa chiyani anthu anasankha December 25 kuti likhale tsiku la Khirisimasi?

Popeza palibe umboni wosonyeza kuti Yesu Khristu anabadwa pa December 25, n’chifukwa chiyani anthu amachitabe Khirisimasi pa detili? Buku lina (Encyclopædia Britannica) limanena kuti atsogoleri achipembedzo ayenera kuti anasankha detili “kuti lizigwirizana ndi chikondwerero chachikunja chachiroma chimene ankachita pokondwerera kuwala kwa dzuwa lamphamvu” m’nthawi yozizira. Buku linanso limati akatswiri ambiri amaphunziro amakhulupirira kuti anthu anasankha tsiku limeneli “pofuna kuti anthu achikunja amene analowa Chikhristu aziona kuti ndi chosangalatsa.”​—The Encyclopedia Americana.