Yankho la m’Baibulo

Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti “Mulungu adzaweruza adama.” (Aheberi 13:4) Mawu achigiriki akuti por·neiʹa amene anawamasulira kuti “dama” amatanthauzanso kugonana kwa anthu amene sanakwatirane. Choncho, Mulungu amaona kuti ndi tchimo ngati anthu amene sanakwatirane akukhalira limodzi, ngakhale kuti anthuwo akuona kuti adzakwatirana m’tsogolo.

Nanga bwanji ngati mwamuna ndi mkaziyo akukondana kwambiri? Mulungu amafunabe kuti anthu akwatirane asanayambe kugonana. Potilenga, Mulungu anatipatsa mphatso yoti tizitha kukondana. Ndipotu khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. (1 Yohane 4:8) Choncho, Mulungu ali ndi chifukwa chomveka chimene amanenera kuti anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kumagonana.