Yankho la m’Baibulo

Popemphera mukhoza kutchula chinthu chilichonse chogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Pa mfundo imeneyi, Baibulo limati: “Chilichonse chimene tingamupemphe [Mulungu] mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Kodi muyenera kutchulanso mavuto anu? Inde. Baibulo limati: “Mukhuthulireni [Mulungu] za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.

Zinthu zimene tingapemphe

  • Kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu.—Luka 17:5.

  • Kuti mzimu woyera, kapena kuti mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito, uzitithandiza kuchita zabwino.—Luka 11:13.

  • Kuti atipatse mphamvu zoti tithe kulimbana ndi mavuto athu komanso tipirire mayesero.—Afilipi 4:13.

  • Kuti atipatse mtendere wamumtima.—Afilipi 4:6, 7.

  • Kuti atipatse nzeru zotithandiza kuti tizitha kusankha bwino zochita.—Yakobo 1:5.

  • Kuti atipatse zinthu zofunikira pa moyo wa tsiku ndi tsiku.—Mateyu 6:11.

  • Kuti atikhululukire machimo athu.—Mateyu 6:12.