Pitani ku nkhani yake

Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?

Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Mzimu woyera ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito. (Mika 3:8; Luka 1:35) Mulungu amatumiza mzimu wake, kapena kuti mphamvu zake, pamalo alionse amene iyeyo wafuna n’cholinga choti achite zimene akufuna.​—Salimo 104:30; 139:7.

 Mawu a m’Baibulo akuti “mzimu” anamasuliridwa kuchokera kumawu achiheberi akuti ruʹach ndiponso achigiriki akuti pneuʹma. Nthawi zambiri mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito ponena za mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito, kapena kuti mzimu woyera. (Genesis 1:2) Komabe, mawuwa anagwiritsidwanso ntchito m’Baibulo ponena za zinthu zina:

 Mawu onsewa akufanana chifukwa akufotokoza zinazake zimene anthu sangathe kuziona. Komabe, zinthu zimenezi zimachita zinthu zimene anthu angazione. N’chimodzimodzinso ndi mzimu wa Mulungu. Mzimuwo “uli ngati mphepo ndipo anthu sangathe kuuona kapena kuukhudza, koma ndi wamphamvu kwambiri.”​—An Expository Dictionary of New Testament Words, by W. E. Vine.

 M’Baibulo, mzimu woyera nthawi zina umatchulidwa kuti ndi “manja” kapena “zala” za Mulungu. (Salimo 8:3; 19:1; Luka 11:20; yerekezerani ndi Mateyu 12:28.) Munthu waluso amapanga ndi kukonza zinthu zosiyanasiyana ndi manja komanso zala zake. Nayenso Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti zinthu zotsatirazi zichitike:

Mzimu woyera si munthu

 Baibulo limasonyeza kuti mzimu woyera si munthu chifukwa linauyerekezera ndi “manja,” “zala” ndiponso “mpweya.” (Ekisodo 15:8, 10) Manja a munthu waluso sangagwire ntchito pawokha popanda bongo ndi thupi. Nawonso mzimu woyera wa Mulungu umagwira ntchito yokhayo imene Mulunguyo wafuna kuti ichitike. (Luka 11:13) Baibulo limayerekezeranso mzimu wa Mulungu ndi madzi. Komanso limasonyeza zoti munthu amene ali ndi mzimu woyera amakhala ndi chikhulupiriro ndiponso amakhala wodziwa zinthu. Mfundo zonsezi zikusonyeza kuti mzimu woyera si munthu.​—Yesaya 44:3; Machitidwe 6:5; 2 Akorinto 6:6.

 Baibulo limatiuza mayina a Yehova Mulungu ndi a Mwana wake Yesu Khristu, koma silitiuza zoti mzimu woyera uli ndi dzina. (Yesaya 42:8; Luka 1:31) Pa nthawi ina, Sitefano yemwe anali Mkhristu woyamba kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake, anaona masomphenya a kumwamba. M’masomphenyawo, iye anaona anthu awiri okha osati atatu. Baibulo limati: “Iye, pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyera, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelero wa Mulungu ndi wa Yesu ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu.” (Machitidwe 7:55) Apa Mulungu anagwiritsa ntchito mphamvu ya mzimu woyera kuti athandize Sitefano kuona masomphenyawa.

Zimene anthu ena amanena zokhudza mzimu woyera

 Zimene anthu ena amanena: Mzimu woyera ndi munthu ndipo uli m’gulu la anthu atatu amene apanga Mulungu m’modzi, monga mmene limasonyezera lemba la 1 Yohane 5:7, 8, m’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

 Zoona zake: M’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu muli mawu otsatirawa pa 1 Yohane 5:7, 8: “Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi. Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.” Koma akatswiri ofufuza apeza kuti mawu amenewa sanalembedwe ndi mtumwi Yohane ndipo si a m’Baibulo. Pa nkhaniyi pulofesa wina wotchedwa Bruce M. Metzger analemba kuti: “Mawu amenewa anangowonjezeredwa ndipo si oona. Sakuyenera ngakhale pang’ono kukhala m’Chipangano Chatsopano.”​—A Textual Commentary on the Greek New Testament.

 Zimene anthu ena amanena: Baibulo limatchula mzimu ngati munthu. Umenewu ndi umboni wakuti mzimu woyera ndi munthu.

 Zoona zake: N’zoona kuti nthawi zina Baibulo limatchula mzimu woyera ngati munthu, koma zimenezi si umboni wakuti mzimu woyerawo ndi munthu. Kumbukirani kuti Baibulo limatchulanso nzeru, imfa ndiponso uchimo ngati anthu. (Miyambo 1:20; Aroma 5:17, 21) Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza kuti nzeru ili ndi “ntchito zake” komanso “ana ake.” Baibulo lomweli likusonyezanso kuti uchimo umachita zinthu ngati kunyenga anthu, kuwapha komanso kuwachititsa kusirira zinthu mwansanje.​—Mateyu 11:19, Buku Lopatulika; Luka 7:35, Buku Lopatulika; Aroma 7:8, 11.

 Mofanana ndi zimenezi, pamene mtumwi Yohane ankalemba mawu amene Yesu analankhula, anatchula mzimu woyera ngati munthu. Iye anati mzimuwo ndi “mthandizi” amene adzapereka umboni, adzatsogolera, adzalankhula, adzamva, adzalengeza, adzalemekeza ndiponso adzalandira. Ponena za “mthandizi” ameneyu, mtumwi Yohane anagwiritsa ntchito mawu otchulira munthu, monga akuti “iye” komanso “amene.” (Yohane 16:7-15) Mtumwi Yohane anachita zimenezi chifukwa chakuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “mthandizi” (pa·raʹkle·tos) angagwiritsidwenso ntchito ponena za munthu wamwamuna, ndipo malinga ndi malamulo a chinenero cha Chigiriki, mawuwa anafunika kuyendera limodzi ndi mawu otchulira munthu, monga akuti “iye” kapena “amene.” Ponena za mzimu woyera womwewu, nthawi zina Yohane ankagwiritsa ntchito mawu ena achigiriki (pneuʹma) amene ngati atagwiritsidwa ntchito ponena za munthu, sasonyeza kuti munthuyo ndi mwamuna kapena mkazi. Pamalo onse amene Yohane analemba mawu amenewa, anagwiritsira ntchito mawu ena amene sangagwiritsidwe ntchito ponena za munthu, monga akuti “umenewo.”—Yohane 14:16, 17.

 Zimene anthu ena amanena: Anthu akamabatizidwa m’dzina la mzimu woyera zimasonyeza kuti mzimu woyerawo ndi munthu.

 Zoona zake: M’Baibulo, nthawi zina mawu akuti “dzina” amaimira mphamvu kapena ulamuliro. (Deuteronomo 18:5, 19-22; Esitere 8:10) Zimenezi zingafanane ndi zimene anthu ena anganene potsimikiza kuti zimene akunenazo n’zoona. Iwo anganene kuti ndikutsimikiza “m’dzina la chilamulo.” Munthu amene wabatizidwa “m’dzina la ” mzimu woyera anazindikira mphamvu ya mzimu woyera imene Mulungu amaigwiritsa ntchito pochita zimene akufuna.—Mateyu 28:19.

 Zimene anthu ena amanena: Atumwi a Yesu ndiponso ophunzira ena oyambirira ankakhulupirira kuti mzimu woyera ndi munthu.

 Zoona zake: Baibulo komanso mbiri yakale sifotokozapo zimenezo. Pa nkhaniyi, buku lina limati: “Zoti Mzimu Woyera ndi Munthu wopatulika . . . Zinayamba m’chaka cha 381 A.D., pa msonkhano wa akuluakulu a Tchalitchi umene unachitika ku Constantinople.” (The Encyclopædia Britannica) Apa n’kuti patapita zaka zoposa 250 atumwi onse atamwalira.