Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?

Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?

Yankho la m’Baibulo

 Inde, tikutero chifukwa Mulungu amasintha maganizo ake pa zimene amafuna kuchitira anthu, iwo akasintha khalidwe lawo. Mwachitsanzo, Mulungu atauza Aisiraeli kuti adzawalanga, ananenanso kuti: “Mwina adzamvera ndipo aliyense wa iwo adzabwerera kuchoka panjira yake yoipa. Pamenepo ndidzasintha maganizo anga pa tsoka limene ndikufuna kuwagwetsera chifukwa cha zochita zawo zoipa.”—Yeremiya 26:3.

 Omasulira Mabaibulo ambiri anamasulira lembali ngati kuti Mulungu “angalape” chifukwa cha chilango chomwe ankafuna kupereka kwa Aisiraeli. Ndipo zimenezi zingasonyeze kuti Mulungu analakwitsa. Komabe mawu Achiheberi choyambirira a palembali, angatanthauze “kusintha maganizo kapena zimene umafuna kuchita.” Pulofesa wina ananena kuti: “Munthu akasintha khalidwe lake, zimapangitsa kuti Mulungu asinthe chilango chomwe amafuna kumupatsa.”

 Ngakhale kuti Mulungu angasinthe maganizo ake sizikutanthauza kuti n’zimene ayenera kuchita nthawi zonse. Taonani nkhani zina za m’Baibulo zosonyeza kuti Mulungu sanasinthe maganizo ake:

  •   Mulungu sanalole kuti Balaki amuchititse kusintha maganizo Ake pa nthawi imene Balakiyo ankafuna kuti Mulungu atemberere mtundu wa Aisiraeli.​—Numeri 23:18-20.

  •   Sauli, yemwe anali Mfumu ya Aisiraeli atayamba kuchita zoipa, Mulungu sanasinthe maganizo ake atanena kuti amusiyitsa kulamulira monga mfumu ya Aisiraeli.​—1 Samueli 15:28, 29.

  •   Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake lakuti Mwana wake adzakhala wansembe mpaka kalekale. Iye sadzasintha maganizo ake pankhaniyi.​—Salimo 110:4.

Kodi si paja Baibulo limati Mulungu sasintha?

 Inde, ndipotu limati Mulungu ananena kuti: ‘Ine ndine Yehova, sindisintha.’ (Malaki 3:6) Komanso Baibulo limanena kuti Mulungu “sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yakobo 1:17) Kodi zimenezi zikutsutsana ndi zimene Baibulo limanena zakuti Mulungu amasintha maganizo ake? Ayi, tikutero chifukwa chakuti Mulungu sasintha mmene alili komanso mfundo zake zachikondi ndi chilungamo zomwe amayendera sizisintha. (Deuteronomo 32:4; 1 Yohane 4:8) Komabe, angapatse anthu malangizo osiyanasiyana pa nthawi zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Mulungu anapatsa Mfumu Davide malangizo osiyana a mmene angamenyere nkhondo ziwiri zotsatizana. Komatu malangizo onsewa anathandiza.​—2 Samueli 5:18-25.

Kodi Mulungu amadziimba mlandu chifukwa choti analenga anthu?

 Ayi, koma iye amamva chisoni chifukwa chakuti anthu ambiri amakana kumumvera. Baibulo limafotokoza mmene Mulungu anamvera Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike. Limati: “Chotero, Yehova anamva chisoni kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.” (Genesis 6:6) Palembali, mawu akuti “anamva chisoni,” anachokera ku mawu Achiheberi omwe angatanthauzenso “kusintha maganizo.” Choncho, Mulungu anasintha maganizo ake n’kuwononga anthu ambiri omwe analiko Chigumula chisanachitike chifukwa chakuti anthuwo anali oipa. (Genesis 6:5, 11) Ngakhale kuti anakhumudwa kwambiri chifukwa chakuti anthu ambiri anasankha kuchita zoipa, iye sanasinthe maganizo ake okhudza anthu onse. N’chifukwa chake anapulumutsa Nowa ndi banja lake pa nthawi ya Chigumula kuti anthu asatheretu padziko lapansi.​—Genesis 8:21; 2 Petulo 2:5, 9..