Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Alipodi?

Kodi Mulungu Alipodi?

Yankho la m’Baibulo

 Inde, ndipo m’Baibulo muli umboni wamphamvu wotsimikizira kuti Mulungu alipodi. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza” komanso “nzeru” pokhulupirira Mulungu, osati kumangokhulupirira zilizonse zimene zipembedzo zinganene. (Aroma 12:1; 1 Yohane 5:20) Tiyeni tigwiritsire ntchito “luntha la kuganiza” komanso “nzeru” pokambirana mfundo zotsatirazi zochokera m’Baibulo:

  •   Zinthu zonse za m’chilengedwechi zinasanjidwa mwadongosolo kwambiri, ndipo zina ndi zamoyo. Zimenezi zikusonyeza kuti pali winawake amene anazilenga. Baibulo limati: “N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheberi 3:4) Ngakhale kuti mawu a palembali ndi osavuta kumva, anthu ochuluka ophunzira kwambiri amaona kuti mfundo ya pavesili ndi yamphamvu. a

  •   Anthufe mwachibadwa tili ndi mtima wofuna kudziwa cholinga cha moyo wathu. Mtima umenewu umatichititsa kuti tizimva ngati tili ndi njala inayake, osati yofuna kudya chakudya chenicheni, koma cha mtundu wina. Baibulo limanena kuti mtima umenewu ndi mbali ya “zosowa zathu zauzimu,” ndipo umatichititsa kuti tizifunitsitsa kumudziwa Mulungu komanso kumulambira. (Mateyu 5:3; Chivumbulutso 4:11) Mtima womwe tili nawowu ndi umboni wakuti Mulungu alipodi komanso kuti iyeyo ndi Mlengi wachikondi amene amafuna kuti ifeyo tikhale naye pa ubwenzi.—Mateyu 4:4.

  •   M’Baibulo muli maulosi ofotokoza zinthu mwatsatanetsatane amene analembedwa kale kwambiri koma anakwaniritsidwa ndendende mmene analembedwera. Zimenezi zimatipatsa umboni wamphamvu wosonyeza kuti maulosiwo sanachokere kwa munthu ayi, koma kwa winawake wamphamvu kuposa anthu.—2 Petulo 1:21.

  •   Anthu amene anagwiritsidwa ntchito polemba Baibulo ankadziwa zinthu zina zokhudzana ndi sayansi zimene anthu a m’nthawiyo sankazidziwa. Mwachitsanzo, kale anthu ambiri ankakhulupirira zoti dziko lapansili lili pamsana pa nyama inayake, monga njovu, nguluwe kapena ng’ombe. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limati Mulungu “anakoloweka dziko lapansi m’malere.” (Yobu 26:7) Komanso Baibulo linanena molondola pa nkhani zokhudza mmene dziko lapansi lilili, kuti ndi “lozungulira.” (Yesaya 40:22) Anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu amene analemba nawo Baibulowo ankadziwa zinthu zakuya zokhudzana ndi sayansi zimenezi chifukwa choti anauzidwa ndi Mulungu.

  •   Baibulo limayankha mafunso ambirimbiri ovuta, ndipo anthu ena akalephera kupeza mayankho ogwira mtima a mafunso amenewo amasiya kukhulupirira Mulungu. Mwachitsanzo: Ngati Mulungu ali ndi chikondi komanso ndi wamphamvu yonse, n’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika zinthu zambiri zoipa komanso anthu ambiri akuvutika? N’chifukwa chiyani nthawi zambiri zipembedzo zimalimbikitsa zinthu zoipa m’malo mwa zinthu zabwino?—Tito 1:16.

a Mwachitsanzo, ponena za chilengedwechi, malemu Allan Sandage yemwe anali katswiri wa sayansi ya zinthu zakuthambo, anati: “Ndikuona kuti n’zosatheka kuti zinthu zadongosolo zimene zili m’chilengedwechi zinangokhalako mwangozi. Payenera kukhala winawake amene anazisanja bwino chonchi. Ineyo sindimudziwa Mulungu. Komabe ndimakhulupirira mfundo yakuti pali winawake amene analenga zinthuzi, mosiyana ndi anthu amene amati chilengedwechi chinangokhalako chokha.”