Pitani ku nkhani yake

Kodi Mdyerekezi Alipodi?

Kodi Mdyerekezi Alipodi?

Yankho la m’Baibulo

 Inde Mdyerekezi alipodi. Iye ndi “wolamulira wa dziko,” mngelo amene anakhala woipa ndipo sanamvere Mulungu. (Yohane 14:30; Aefeso 6:11, 12) Baibulo limasonyeza zochita za Mdyerekezi kudzera m’matanthauzo a mayina ake otsatirawa:

Mdyerekezi si uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu

 Anthu ena amaganiza kuti Mdyerekezi ndi khalidwe la uchimo limene limakhala mumtima mwa munthu. Koma Baibulo limanena kuti nthawi ina Mulungu analankhula ndi Satana. Mulungu alibe uchimo ndiye sizikanatheka kuti azilankhula ndi uchimo umene unali mumtima mwake. (Deuteronomo 32:4; Yobu 2:1-6) Komanso Satana anayesapo Yesu amene alibe uchimo. (Mateyu 4:8-10; 1 Yohane 3:5) Choncho Baibulo limasonyeza kuti Mdyerekezi alipodi ndipo si uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu.

 Kodi tiyenera kudabwa tikamaona kuti anthu ambiri amakhulupirira kuti kulibe Mdyerekezi? Ayi, chifukwatu Baibulo limanena kuti Satana amagwiritsira ntchito njira zachinyengo kuti zolinga zake zitheke. (2 Atesalonika 2:9, 10) Njira yaikulu imene Satana amapusitsira anthu n’kuwachititsa kuti azikhulupirira kuti iyeyo kulibe.—2 Akorinto 4:4.

Zinthu zabodza zimene anthu ena amakhulupirira zokhudza Mdyerekezi

  Zimene anthu ena amakhulupirira: Dzina lina la Mdyerekezi ndi Lusifara.

 Zoona zake: Liwu la Chiheberi limene m’Mabaibulo ena amalimasulira kuti “Lusifara” limatanthauza “wonyezimira.” (Yesaya 14:12) Nkhani imene ili m’chaputalachi ikusonyeza kuti mawu amenewa amatanthauza mafumu a Babulo amene Mulungu ananena kuti adzawachititsa manyazi chifukwa cha kudzikuza kwawo. (Yesaya 14:4, 13-20) Mawu akuti “wonyezimira” anagwiritsidwa ntchito m’njira yoseka mafumu a Babulo pamene anagonjetsedwa.

  Zimene anthu ena amakhulupirira: Mulungu amagwiritsira ntchito Satana pofuna kulanga anthu.

 Zoona zake: Mdyerekezi ndi mdani wa Mulungu osati mtumiki wake. Satana Mdyerekezi amazunza komanso kunenera mabodza anthu amene amatumikira Mulungu.—1 Petulo 5:8; Chivumbulutso 12:10.