Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Masoka Achilengedwe N’chilango Chochokera kwa Mulungu?

Kodi Masoka Achilengedwe N’chilango Chochokera kwa Mulungu?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo silimaphunzitsa zoti Mulungu ndi amene akuchititsa masoka achilengedwe amene akuchitika masiku ano. Chiweruzo chimene Mulungu amapereka, chomwe chafotokozedwa m’Baibulo, n’chosiyana kwambiri ndi masoka achilengedwe.

  1. Mulungu sawononga anthu abwino pamodzi ndi oipa. Baibulo limati: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”—1 Samueli 16:7.

  2. Yehova amaona mumtima mwa munthu aliyense payekha ndipo amawononga anthu okhawo amene iye waona kuti ndi oipa.—Genesis 18:23-32.

  3. Mulungu asanawononge anthu, amayamba wawachenjeza kaye. Zimenezi zimapereka mpata kwa anthu amene angamvetsere kuti asawonongedwe.

Mosiyana ndi zimenezi, nthawi zambiri masoka achilengedwe akamachitika sipakhala chenjezo lililonse, ndipo anthu amene amafa kapena kuvulala pa masokawa amakhala abwino ndi oipa omwe. Komanso zochita za anthu n’zimene zikuchititsa kuti masoka achilengedwewa azikhala oopsa kwambiri masiku ano. Izi zili choncho chifukwa anthu awononga chilengedwe komanso akumanga nyumba m’madera amene mumakonda kuchitika masoka monga zivomerezi ndiponso kusefukira kwa madzi.

Onaninso

NSANJA YA OLONDA

Masoka Achilengedwe Kodi Ndi Umboni Wakuti Mulungu Ndi Wankhanza?

Ngatidi Mulungu amadana ndi zoipa, n’chifukwa chiyani amalola kuti anthu osalakwa azifa chifukwa cha masoka achilengedwe?