Kodi Dzina la Mulungu Ndi Yesu?
Yankho la m’Baibulo
Yesu ananena kuti iye ndi “Mwana wa Mulungu.” (Yohane 10:36; 11:4) Yesu sananenepo kuti iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse.
Komanso, Yesu anapemphera kwa Mulungu. (Mateyu 26:39) Pamene ankaphunzitsa otsatira ake kupempherera, Yesu anati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”—Mateyu 6:9.
Yesu anatchula dzina la Mulungu pamene ananena mawu ochokera m’Chilamulo kuti: “Tamverani Aisiraeli inu, Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.”—Maliko 12:29; Deuteronomo 6:4.