Pitani ku nkhani yake

Kodi Halowini Inayamba Bwanji, Ndipo Baibulo Limati Chiyani pa Nkhaniyi?

Kodi Halowini Inayamba Bwanji, Ndipo Baibulo Limati Chiyani pa Nkhaniyi?

Yankho la m’Baibulo

M’Baibulo mulibe mawu akuti Halowini. Chiyambi cha Halowini komanso miyambo imene anthu amachita masiku ano zimasonyeza kuti anthu amachita mwambowu chifukwa cha zikhulupiriro zabodza zokhudza akufa, mizimu komanso ziwanda.​—Onani kamutu kakuti  “Chiyambi cha Halowini komanso miyambo yake.”

Baibulo limachenjeza kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wofunsira kwa mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa.” (Deuteronomo 18:​10-12) Anthu ena amaona kuti Halowini ndi mwambo wongosangalatsa basi. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti zimene zimachitika pamwambowu n’zoipa. Palemba la 1 Akorinto 10:​20, 21, Baibulo limati: “Sindikufuna kuti mukhale ogawana ndi ziwanda. Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova komanso za m’kapu ya ziwanda.”

 Chiyambi cha Halowini komanso miyambo yake

  1. Mwambo wa Samhain: Halowini inachokera ku “chikondwerero chachikunja chimenechi chomwe chinkachitidwa ndi Aselote zaka zoposa 2,000 zapitazo. Iwo ankakhulupirira kuti nthawi ya mwambo wa Samhain ndi imene anthu akufa ankayendayenda padziko n’kumacheza ndi anthu amoyo.” (The World Book Encyclopedia) Koma Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti akufa “sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Choncho n’zosatheka kuti anthu akufa azicheza ndi anthu amoyo.

  2. Zovala ndiponso maswiti: Buku lakuti Halloween​—An American Holiday, An American History, limanena kuti Aselote ankavala zophimba kumaso zoopsa kuti mizimu yoipa izipusitsika n’kumawaona ngati nawonso ndi mizimu n’cholinga choti isawavulaze. Ena ankainyengerera ndi maswiti. Kalekale kwambiri, Atsogoleri achipembedzo cha Katolika a ku Ulaya anatengera miyambo yachikunjayi. Iwo ankauza anthu a tchalitchi chawo kuti azipita kunyumba za anthu n’kumakapempha mphatso. Komatu Baibulo sililola kuti anthu aziphatikiza ziphunzitso zabodza za chipembedzo polambira Mulungu.​—2 Akorinto 6:17.

  3. Mizukwa ndiponso afiti: Kwa nthawi yaitali, anthu akhala akukhulupirira kuti zinthu zimenezi zimakhala kudziko lamizimu. (Halloween Trivia) Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti tizipewa komanso kudana ndi chilichonse chokhudzana ndi mizimu yoipa.​—Aefeso 6:12.

  4. Maungu a pamwambo wa Halowini: Kalekale ku Britain, “anthu amapemphero ankapita kunyumba za anthu n’kumawauza kuti awapatse chakudya n’cholinga choti apempherere anthu amene anamwalira,” ndipo ankayenda ndi dzungu lobowola. Kenako amayatsa kandulo n’kuika mkati mwa dzungulo. Ena amakhulupirira kuti kandulo yemwe anali mkati mwa dzungulo ankaimira mzimu wa munthu womwe uli ku purigatoriyo.” (Halloween​—From Pagan Ritual to Party Night) Ena amanena kuti makandulo okhala m’kati mwa maungu obowolawo ankathamangitsa mizimu yoipa. M’zaka za m’ma 1800 kumpoto kwa America, maungu ankapezeka mosavuta komanso anali osavuta kuboola, n’chifukwa chake ankawagwiritsa ntchito. Anthu ankachita mwambo umenewu chifukwa cha zikhulupiriro zakuti mzimu suufa, munthu amapita kupurigatoriyo komanso kupempherera anthu amene anamwalira. Zikhulupiriro zonsezi ndi zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena.​—Ezekieli 18:4.