Pitani ku nkhani yake

Kodi Chilombo cha Mitu 7 Chotchulidwa M’buku la Chivumbulutso Chaputala 13, Chikuimira Chiyani?

Kodi Chilombo cha Mitu 7 Chotchulidwa M’buku la Chivumbulutso Chaputala 13, Chikuimira Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Chilombo cha mitu 7 chimene chatchulidwa palemba la Chivumbulutso 13:1 chikuimira ndale za padziko lonse.

  •   Chilombochi chili ndi ulamuliro, mphamvu komanso mpando wachifumu ndipo zimenezi zikusonyeza kuti chikuimira ndale.​—Chivumbulutso 13:2.

  •   Chimalamulira “anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chinenero chilichonse ndi dziko lililonse,” zomwe zikusonyeza kuti chilombochi sichikuimira boma landale limodzi lokha.​—Chivumbulutso 13:7.

  •   Chili ndi maonekedwe a zilombo 4 zimene zafotokozedwa palemba la Danieli 7:2-8, kuphatikizapo maonekedwe ofanana ndi kambuku, mapazi ofanana ndi chimbalangondo, kamwa yofanana ndi ya mkango, ndi nyanga 10. Zilombo zimene zatchulidwa mu ulosi wa Danieli zikuimira mafumu, kapena maulamuliro andale amene amalamulira motsatizana. (Danieli 7:17, 23) Choncho chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso chaputala 13 chikuimira maulamuliro onse andale padziko lapansi pano.

  •   Chilombochi “chikutuluka m’nyanja,” kusonyeza kuti chikuchokera m’mitundu ya anthu ambirimbiri omwe amapanga maulamuliro andale.​—Chivumbulutso 13:1; Yesaya 17:12, 13.

  •   Baibulo limanena kuti nambala, kapena kuti dzina la chilombo lakuti 666 ndi “nambala ya munthu.” (Chivumbulutso 13:17, 18) Mawu amenewa akusonyeza kuti chilombo chimene chinatchulidwa pa Chivumbulutso chaputala 13 ndi gulu la anthu, osati gulu la mizimu kapena ziwanda.

 Ngakhale kuti maulamuliro andale amasiyana pa zinthu zina, ndi ofanana m’njira yakuti onse amayesetsa kuti azilamulirabe m’malo modzipereka ku ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. (Salimo 2:2) Iwo adzagwirizana kumenyana ndi gulu lankhondo la Mulungu limene liti lidzatsogoleredwe ndi Yesu Khristu pa Aramagedo komabe magulu onse andale adzawonongedwa pankhondoyi.​—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:19, 20.

“Nyanga 10 ndi mitu 7”

 Manambala ena m’Baibulo amaimira zinthu zina. Mwachitsanzo, 10 ndi 7 amaimira chinthu chokwanira. “Chifaniziro cha chilombo” chimene chinatchulidwa m’buku la Chivumbulutso chingatithandize kumvetsa mokwanira zimene chilombo cha “nyanga 10 ndi mitu 7” chotchulidwa pa Chivumbulutso chaputala 13 chimaimira. (Chivumbulutso 13:​1, 14, 15; 17:3) Baibulo limanena kuti mitu 7 ya chilombo chofiira imaimira “mafumu 7,” kapena maulamuliro.​—Chivumbulutso 17:9, 10.

 Mofanana ndi zimenezi, mitu 7 ya chilombo chimene chinatchulidwa pa Chivumbulutso 13:1 ikuimira maulamuliro 7. Maulamulirowa, omwe ndi Iguputo, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Roma, komanso Britain ndi America, akhala amphamvu kwambiri kwa nthawi yaitali ndipo amatsogolera pozunza anthu a Mulungu. Ngati tingaphere mphongo ponena kuti nyanga 10 zikuimira maboma onse, ang’onoang’ono ndi akuluakulu omwe, ndiye kuti chisoti chachifumu chimene chili panyanga iliyonse chikusonyeza kuti ulamuliro uliwonse umalamulira limodzi ndi ulamuliro wamphamvu kwambiri umene ulipo pa nthawiyo.