Pitani ku nkhani yake

Kodi Chilombo Chofiira Kwambiri Chomwe Chimatchulidwa M’chaputala 17 cha Chivumbulutso Chimaimira Chiyani?

Kodi Chilombo Chofiira Kwambiri Chomwe Chimatchulidwa M’chaputala 17 cha Chivumbulutso Chimaimira Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Chilombo chofiira kwambiri chimene chimatchulidwa m’chaputala 17 cha buku la Chivumbulutso, si chenicheni koma chimaimira bungwe lomwe cholinga chake n’kugwirizanitsa komanso kuimira mayiko onse a padzikoli. Poyamba bungweli linkadziwika kuti League of Nations ndipo panopa limadziwika kuti United Nations.

Kodi chilombo chimenechi tingachidziwe bwanji?

 1. Ndi bungwe landale. Chilombo chofiira kwambiri chili ndi “mitu 7” yomwe akuimira “mapiri 7” ndiponso “mafumu 7” kapena kuti olamulira amphamvu. (Chivumbulutso 17:9, 10) Nthawi zina Baibulo likamanena za maboma limagwiritsa ntchito mawu akuti mapiri komanso zilombo.​—Yeremiya 51:24, 25; Danieli 2:44, 45; 7:17, 23.

 2. Ndi bungwe lolamulira padziko lonse. Chilombo chofiira kwambirichi chikufanana ndi chilombo cha mitu 7 chotchulidwa mu Chivumbulutso chaputala 13 chomwe chimaimira maboma a padziko lapansi. Zilombo zonsezi zili ndi mitu 7, nyanga 10 ndiponso mayina onyoza Mulungu. (Chivumbulutso 13:1; 17:3) N’zochititsa chidwi kuti zilombo ziwirizi n’zofanana chonchi. Chilombo chofiira kwambiri ndi chifaniziro chabe cha maboma a padziko lapansi.​—Chivumbulutso 13:15.

 3. Limapatsidwa mphamvu ndi maboma. Chilombo chofiira kwambirichi ‘chinatuluka’ kapena kuti chinapatsidwa mphamvu ndi maboma olamulira padziko lapansi.​—Chivumbulutso 17:11, 17.

 4. Limagwirizana ndi zipembedzo. Baibulo limasonyeza kuti Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonse zabodza, wakhala pamsana pa chilombo chofiira kwambiri. Zimenezi zikusonyeza kuti bungweli limagwirizana kwambiri ndi zipembedzo.​—Chivumbulutso 17:3-5.

 5. Limanyoza Yehova. Chilombochi ndi “chodzaza ndi mayina onyoza Mulungu.”​—Chivumbulutso 17:3.

 6. Chinasiya Kugwira Ntchito kwa Kanthawi. Chilombo chofiira kwambiri chidzapita “kuphompho” * kapena kuti sichidzagwira ntchito kwa kanthawi. Koma kenako chidzatuluka n’kuyamba kugwiranso ntchito.​—Chivumbulutso 17:8.

Zimene Baibulo linaneneratu zikukwaniritsidwa

Tsopano tiyeni tione mmene bungwe la United Nations, limene poyamba linkatchulidwa kuti League of Nations, lakwaniritsira ulosi wa m’Baibulo wokhudza chilombo chofiira kwambiri.

 1. Ndi bungwe landale. Bungwe la United Nations limanena kuti dziko lililonse lomwe ndi membala wake ndi “lofanana ndi linzake ndipo onse ali ndi mphamvu zofanana.” *

 2. Ndi bungwe lolamulira padziko lonse. Mu 2011, bungwe la United Nations linali ndi mamembala 193. Bungweli ndi limene lili ndi mamembala ochuluka kwambiri, choncho lili ndi mphamvu padziko lonse.

 3. Limapatsidwa mphamvu ndi maboma. Mayiko omwe ali m’bungweli ndi amene amathandiza kuti bungweli lizipitirizabe kugwira ntchito komanso ndi amene amalipatsa mphamvu.

 4. Limagwirizana ndi zipembedzo. Zipembedzo zapadzikoli zakhala zikuthandiza bungwe la League of Nations ndiponso United Nations. *

 5. Limanyoza Yehova. Bungwe la United Nations “linapangidwa n’cholinga chokhazikitsa mtendere padziko lonse lapansi.” * Ngakhale kuti cholinga chimenechi chingaoneke chothandiza, bungweli limanyoza Yehova chifukwa limanena kuti likhoza kuchita zinthu zimene Mulungu ananena zoti ndi Ufumu wake wokha umene ungazichite.​—Salimo 46:9; Danieli 2:44.

 6. Linasiya kugwira ntchito kwa kanthawi. Bungwe la League of Nations linakhazikitsidwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha n’cholinga chokhazikitsa mtendere. Bungweli linalephera kukwaniritsa zimenezi ndipo linatha pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba mu 1939. Ndiyeno nkhondo yachiwiri itatha mu 1945 panapangidwa bungwe la United Nations. Mmene bungweli linapangidwira ndiponso zochita zake sizinasiyane ndi bungwe la United Nations.

^ ndime 10 Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linamasulira mawu akuti “phompho” kuti ndi dzenje lopanda malire. (Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words) Pomwe Baibulo la King James Version linamasulira kuti “dzenje lopanda pothera.” Koma Baibulo likamanena za mawu amenewa limakhala likutanthauza malo amene chinthu sichingathe kuchita chilichonse.

^ ndime 13 Onani mutu wachiwiri wa m’chikalata cha malamulo a bungwe la United Nations.

^ ndime 16 Mwachitsanzo, pa msonkhano wina pomwe atsogoleri azipembedzo za Chipulotesitanti anachita ku America mu 1918, ananena kuti bungwe la League of Nations ndi bungwe landale lomwe likuimira Ufumu wa Mulungu padziko lapansi. M’chaka cha 1965, atsogoleri a zipembedzo za Chibuda, Chikatolika, Orthodox, Chihindu,Chisilamu,Chiyuda,Chipulotesitanti anachita msonkhano ku San Francisco n’cholinga choti athandize komanso kupempherera bungwe la United Nations. Mu 1979, Papa Yohane Paulo Wachiwiri, ananena kuti akukhulupirira kuti bungwe la United Nations “lidzakhalabe lamphamvu kwambiri padziko lonse ndipo lidzathandiza pokhazikitsa mtendere ndiponso chilungamo mpaka kalekale.”

^ ndime 17 Onani mutu woyamba wa m’chikalata cha malamulo a bungwe la United Nations.