Pitani ku nkhani yake

Kodi Mdyerekezi Ndi Amene Amachititsa Mavuto Onse?

Kodi Mdyerekezi Ndi Amene Amachititsa Mavuto Onse?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo limasonyeza kuti Satana Mdyerekezi ndi munthu weniweni. Iye ali ngati mtsogoleri wa zigawenga wamphamvu kwambiri amene amagwiritsa ntchito “zizindikiro zabodza” ndiponso “chinyengo” pofuna kukwaniritsa zolinga zake. Ndipotu Baibulo limati iye “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” (2 Atesalonika 2:9, 10; 2 Akorinto 11:14) Zinthu zoipa zimene iye amachita zimapereka umboni wakuti Satanayo alipodi.

Komabe, sikuti Mdyerekezi ndi amene amachititsa mavuto onse. N’chifukwa chiyani tikutero? Mulungu analenga anthu m’njira yakuti azitha kusankha pakati pa chabwino ndi choipa. (Yoswa 24:15) Choncho, tikasankha zinthu mopanda nzeru timakumana ndi mavuto.—Agalatiya 6:7, 8.