Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Ndi Buku la Azungu?

Kodi Baibulo Ndi Buku la Azungu?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo silinalembedwe ndi azungu. Anthu onse amene Mulungu anawagwiritsira ntchito polemba Baibulo anali a ku Asia. Ndipotu, Baibulo silisonyeza kuti mtundu wina wa anthu ndi wapamwamba kuposa mtundu wina. Baibulo limanena kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.