Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yoikidwa Magazi?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yoikidwa Magazi?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limatilamula kuti tisamadye magazi. Choncho, tiyenera kupewa kudya kapena kuikidwa magazi kapena zigawo zake zikuluzikulu. Taonani malemba otsatirawa:

  •   Genesis 9:4. Chigumula chitachitika, Mulungu analola Nowa ndi banja lake kuti azidya nyama koma anawauza kuti asamadye magazi ake. Mulungu anauza Nowa kuti: “Koma musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.” Lamulo limeneli likugwiranso ntchito kwa anthu onse chifukwa tonsefe ndife zidzukulu za Nowa.

  •   Levitiko 17:14. “Musamadye magazi a nyama iliyonse, chifukwa moyo wa nyama ina iliyonse ndi magazi ake. Aliyense wodya magaziwo ayenera kuphedwa.” Mulungu amaona kuti moyo wa nyama ndi wake ndipo uli m’magazi. Ngakhale kuti lamuloli linaperekedwa kwa Aisiraeli okha, likusonyeza kuti Mulungu amaona kuti ndi kulakwa kwambiri kudya magazi.

  •   Machitidwe 15:20. ‘Pewani magazi.’ Lamulo limene Mulungu anapereka kwa Nowa analiperekanso kwa Akhristu. Akatswiri a mbiri yakale amati Akhristu oyambirira ankapewa kudya magazi, ngakhale atagwiritsidwa ntchito ngati mankhwala.

N’chifukwa chiyani Mulungu anatilamula kuti tizipewa magazi?

 N’zoona kuti kuikidwa magazi tikadwala kukhoza kuyambitsa mavuto ena m’thupi. Koma chifukwa chachikulu chopewera magazi n’chakuti Mulungu anatilamula zimenezi chifukwa magazi amaimira moyo womwe ndi wopatulika kwa iye.​—Levitiko 17:11; Akolose 1:20.