Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yogonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Yankho la m’Baibulo

Mulungu analenga anthu m’njira yakuti mwamuna ndi mkazi okwatirana azitha kugonana. (Genesis 1:27, 28; Levitiko 18:22; Miyambo 5:18, 19) Baibulo limaletsa kugonana kwa anthu ena alionse omwe si mwamuna ndi mkazi okwatirana, kaya anthuwo akugonana amuna kapena akazi okhaokha. (1 Akorinto 6:18) Zimenezi zikuphatikizapo kugonana kwenikweni, kuseweretsana maliseche ndiponso kugonana m’kamwa kapena kumatako.

Ngakhale kuti Baibulo limaletsa zoti amuna kapena akazi azigonana okhaokha, silimavomereza zoti anthu azidana ndi anthu amene amachita khalidwe limeneli. M’malomwake, Akhristu akuuzidwa kuti: “Chitirani ulemu anthu onse.”—1 Petulo 2:17, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Kodi munthu angabadwe ndi mtima wofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzake?

Baibulo silimanena mwachindunji zoti munthu angabadwe ndi mtima umenewu kapena ayi, koma limanena kuti tonsefe timabadwa ndi mtima wokonda kuchita zimene Mulungu amaletsa. (Aroma 7:21-25) Ndiponso Baibulo silinena za chimene chimachititsa kuti anthu ena azifuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo koma limaletsa khalidwe limeneli.

Kodi munthu amene ali ndi mtima wofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzake angatani kuti azikondweretsa Mulungu?

Baibulo limati: “Musalole kuti thupi lanu lizikulamulirani. Chititsani ziwalo za thupi lanu kukhala zakufa ku chilakolako chofuna kugonana m’njira yolakwika.” (Akolose 3:5, Contemporary English Version) Kuti munthu achititse ziwalo zake kukhala zakufa ku zilakolako zolakwika, zimene zimachititsa munthu kuchita zinthu zoipa, munthuyo amafunika kulamulira maganizo ake. Ngati nthawi zonse mumaganizira zinthu zabwino, mukhoza kukwanitsa kuthana ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. (Afilipi 4:8; Yakobo 1:14, 15) N’zoona kuti poyamba mungavutike kulimbana ndi maganizo oipawo koma mukhoza kukwanitsa. Mulungu akukulonjezani kuti adzakuthandizani “kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.”—Aefeso 4:22-24.

Amuna komanso akazi ambirimbiri amene amafunitsitsa kusangalatsa Mulungu akuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo polimbana ndi chilakolako chofuna kugonana. Mwachitsanzo, anthu amene sanakwatire kapena kukwatiwa ndipo mwina sadzalowa n’komwe m’banja, kapena amene mkazi kapena mwamuna wawo sangathe kugonana, amayesetsa kulamulira chilakolako chawo chogonana ngakhale kuti amakumana ndi mayesero ambiri. Anthu amenewa amakhala mosangalala. Choncho nawonso anthu amene amakhala ndi chilakolako chofuna kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo angathe kulimbana ndi mtima umenewu ngati akufunadi kusangalatsa Mulungu.—Deuteronomo 30:19.