Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YONATANI

“Palibe Chimene Chingalepheretse Yehova”

“Palibe Chimene Chingalepheretse Yehova”

Tayerekezerani kuti mukuona gulu la asilikali omwe ali kumalo omenyera nkhondo. Malowa ali ndi nthaka youma komanso ya miyala. Ngakhale kuti malowo akuoneka kuti si ochititsa chidwi kwenikweni, asilikaliwo omwe ndi Afilisti aona chinachake chomwe chawachititsa chidwi. Akuona amuna awiri Achiisiraeli ali mbali ina ya chigwa cha mtsinje. Asilikaliwo akungoyang’anitsitsa anthuwo mwachidwi ndipo sakudanso nkhawa. Kwa nthawi yayitali Afilisiti akhala akugonjetsa Aisiraeli. Ndipotu Aisiraeli akafuna kunola zipangizo zawo zakumunda amadalira adani awo omwewo. Apa n’zosachita kufunsa kuti anthu a ku Isiraeliwo sangakhale ndi chida chilichonse choopsa. Komanso pa nthawiyi, anthuwo alipo awiri okha. Ndipo ngakhale atakhala kuti ali ndi zida zokwanira, sizingatheke olo pang’ono kugonjetsa Afilisitiwo. Kenako Afilisitiwo akuyamba kukuwa n’kumanyoza Aisiraeliwo kuti: “Bwerani kuno, ndipo tikukhaulitsani!”​—1 Samueli 13:19-​23; 14:11, 12.

Afilisitiwo sakuganizirako n’komwe kuti zinthu zitembenuka ndipo iwowo ndi amene akhaulitsidwe. Aisiraeli aja akuwoloka chigwa cha mtsinjewo ndipo akukwera mtunda kulowera komwe kuli Afilisitiwo. Chigwacho ndi chachitali, moti akukwera mochita kukwawa m’miyala kulowera komwe kuli asilikali a Afilisitiwo. (1 Samueli 14:13) Apa tsopano Afilisitiwo akuona bwinobwino kuti mwamuna amene watsogolayo ali ndi chida ndipo munthu wina amene akumutsatirayo ndi mtumiki wake womunyamulira zida. Koma kodi mwamunayo analidi ndi cholinga chokaukira gulu la asilikalilo? Ngatidi zinali choncho, kodi amaona kuti n’zotheka kuti iyeyo ndi m’nzakeyo akhoza kugonjetsa gulu la asilikaliwo? Kapena kunali chabe kusaganiza bwino?

Mwamunayo ndi woganiza bwinobwino ndipo ali ndi chikhulupiriro champhamvu. Munthu ameneyu dzina lake ndi Yonatani ndipo zomwe anachita zimatiphunzitsa zambiri masiku ano. Ngakhale kuti panopa sitimenya nkhondo yeniyeni, nkhani ya Yonatani imatithandiza kukhala olimba mtima, okhulupirika komanso kupewa mtima wodzikonda. Ndipo zimenezi n’zomwe zimafunika kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu.​—Yesaya 2:4; Mateyu 26:51, 52.

Anali Mwana Wokhulupirika Komanso Msilikali Wolimba Mtima

Kodi n’chiyani chinalimbitsa mtima Yonatani kuti akalimbane ndi gulu la asilikaliwo? Tiyeni tione kaye mbiri yake. Yonatani anali mwana woyamba wa Sauli, mfumu yoyamba ya Isiraeli. Pamene Sauli ankadzozedwa kukhala mfumu, Yonatani anali wamkulu kale, mwina ali ndi zaka 20 kapena kuposerapo. Zikuoneka kuti Yonatani ankagwirizana kwambiri ndi bambo ake ndipo nthawi zambiri bambo akewo ankamuuza zakukhosi kwawo. Yonatani ankadziwa ndithu kuti bambo ake ndi munthu wamtali, wooneka bwino komanso msilikali wolimba mtima. Koma iye ankaganizira kwambiri makhalidwe abwino omwe bambo akewo anali nawo monga chikhulupiriro komanso kudzichepetsa. Yonatani ankaona kuti mpake kuti Yehova anasankha Sauli kuti akhale mfumu. Nayenso mneneri Samueli ananenapo kuti m’dzikolo munalibe munthu wofanana ndi Sauli.​—1 Samueli 9:​1, 2, 21; 10:20-​24; 20:2.

Yonatani ayenera kuti ankasangalala kukamenya nkhondo yogonjetsa adani a anthu a Yehova, m’nthawi ya ulamuliro wa bambo ake. Nkhondo za nthawi imeneyo si zofanana ndi zomwe anthu amamenya masiku ano chifukwa chosankhana mitundu. Pa nthawiyo Yehova anasankha mtundu wa Aisiraeli kuti uzikamenya nkhondo m’malo mwa iyeyo. Nthawi zambiri anthu omwe ankalambira milungu yonyenga ankalimbana kwambiri ndi Aisiraeli. Mwachitsanzo, Afilisiti omwe ankalambira milungu monga Dagoni, nthawi zonse ankafuna kupondereza komanso kugonjetsa anthu a Yehova.

Yonatani ndi amuna ena achiisiraeli, ankaona kuti kumenya nkhondo, unali utumiki wopatulika kwa Yehova. Ndipo Yehova anadalitsa kwambiri Yonatani chifukwa chochita zinthu mwakhama. Sauli atangokhala mfumu, anasankha mwana wakeyu kuti azitsogolera asilikali 1,000. Nthawi ina Yonatani anatsogolera asilikali kukagonjetsa gulu linalake la asilikali a Afilisiti ku Geba. Ngakhale kuti asilikaliwa analibe zida zokwanira, Yehova anawathandiza kuti apambane. Pofuna kubwezera, Afilisiti anasonkhanitsa gulu lalikulu la asilikali. Izi zinachititsa kuti asilikali a Sauli achite mantha kwambiri. Ena anayamba kuthawa, kubisala ndipo enanso anakhala mbali ya Afilisitiwo. Koma Yonatani sanagwe ulesi ndipo analimbabe mtima.​—1 Samueli 13:2-7; 14:21.

Patsiku limene talitchula koyambirira kuja, Yonatani anangochoka mwakachetechete limodzi ndi mtumiki wake womunyamulira zida. Pamene ankafika ku Mikimasi kukakumana ndi asilikali a Afilisiti, Yonatani anauza mtumiki wake zimene ankafuna kuchita. Anagwirizana kuti adzionetsere kwa asilikali a Afilisitiwo. Ngati Afilisitiwo angakanene kuti akamenyane nawo, chikakhala chizindikiro choti Yehova athandiza atumiki akewo kuti apambane. Nthawi yomweyo mtumikiyo anavomera. Mwina mtumiki wakeyo anavomera chifukwa cha mawu amphamvu omwe Yonatani ananena akuti: “Palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.” (1 Samueli 14:​6-​10) Kodi Yonatani ankatanthauza chiyani pamenepa?

Yonatani ankadziwa bwino mmene Mulungu amachitira zinthu ndi atumiki ake. Iye ankakumbukira kuti nthawi ina m’mbuyomo, Yehova anathandiza anthu ake kugonjetsa adani awo ngakhale kuti adaniwo analipo ambiri. Komanso nthawi zina Yehova ankagwiritsa ntchito munthu mmodzi kuti apulumutse anthu ake. (Oweruza 3:​31; 4:1-​23; 16:23-​30) Yonatani ankadziwa kuti chikhulupiriro ndi chofunika kwambiri osati kuchuluka kwa anthu, mphamvu kapena zida za nkhondo. Popeza kuti anali ndi chikhulupiriro, Yonatani anasiyira Yehova udindo woti awaonetse chizindikiro ngati kunali koyenera kuti iyeyo ndi mtumiki wake amenyane ndi Afilisitiwo. Yehova atawasonyeza chizindikirocho, Yonatani analimba mtima n’kupita kukamenya nkhondo.

Mungaone kuti pali zinthu ziwiri zosonyeza kuti Yonatani anali ndi chikhulupiriro. Choyamba, ankalemekeza kwambiri Yehova Mulungu. Ankadziwa kuti Mulungu Wamphamvuyonse sadalira mphamvu za anthu n’cholinga choti akwaniritse cholinga chake. M’malomwake Yehova amadalitsa atumiki ake omwe akumutumikira mokhulupirika. (2 Mbiri 16:9) Chachiwiri, Yonatani asanayambe kumenya nkhondo, anapempha Yehova kuti amuonetse kaye chizindikiro chosonyeza kuti wavomereza kuti amenyedi nkhondoyo. Masiku ano sitiyembekezera kuti Mulungu ationetse zizindikiro zodabwitsa kuti titsimikize zoti wavomereza zimene tasankha. M’malomwake anatipatsa Mawu ake ouziridwa kuti tizitha kudziwa zimene amafuna. (2 Timoteyo 3:​16, 17) Kodi tikafuna kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu, timayamba tafufuza kaye m’Baibulo? Ngati ndi choncho, ndiye kuti tili ngati Yonatani amene ankalemekeza zimene Mulungu ankafuna m’malo mwa zofuna zake.

Yonatani ndi mtumiki wakeyo anakwera chigwacho mofulumira kulowera komwe kunali adaniwo. Afilistiwo atazindikira kuti anthu awiriwo akubwerera nkhondo, anatumiza asilikali kuti akathane nawo. Afilistiwo anali ndi mwayi woti analipo ambiri komanso anali kumtunda. Choncho sakanavutika kupha amuna awiriwo. Koma Yonatani anayamba kukantha Afilisitiwo mmodzi ndi mmodzi ndipo m’mbuyo mwake mtumiki wake uja ankamalizitsa kupha anthuwo. Pa kanthawi kochepa, anapha asilikali 20 a Afilisiti. Ndipotu Yehova sanasiyire pomwepo kuwathandiza chifukwa Baibulo limanena kuti: “Kenako anthu amene anali kutchire mumsasa ndi anthu onse kumudzi wa asilikaliwo anayamba kunjenjemera. Anthu olanda katundu nawonso anali kunjenjemera, ndipo nthaka inayamba kugwedezeka. Zimenezi zinali zochokera kwa Mulungu.”​—1 Samueli 14:15.

Yonatani ndi mnyamata wake analimbana ndi gulu la asilikali okhala ndi zida

Pa nthawiyo kunali chipwirikiti pakati pa Afilisiti ndipo Sauli ndi amuna omwe anali nawo, ankangoona ali chapatali Afilisitiwo atayamba kuphana okhaokha. (1 Samueli 14:16, 20) Aisiraeli ena nawonso analimba mtima n’kuyamba kumenya nawo nkhondoyo ndipo mwina ankagwiritsa ntchito zida za Afilisiti omwe aphedwa. Tsiku limenelo Yehova anapulumutsa anthu ake. Ndipotu mpaka pano, Yehova sanasinthe. Masiku anonso ngati titakhala ndi chikhulupiriro ngati cha Yonatani ndi mnyamata wake yemwe sadziwika dzina, sitidzanong’oneza bondo kuti tinasankha molakwika kutumikira Mulungu.​—Malaki 3:6; Aroma 10:11.

“Anachita Zimenezi Mothandizidwa ndi Mulungu”

Ngakhale kuti Yonatani zinthu zinamuyendera bwino chonchi, koma sizinakhale choncho ndi Sauli. Sauli sanamvere Samueli, mneneri amene anaikidwa ndi Yehova ndipo anapereka yekha nsembe yomwe ankayenera kuipereka ndi mneneri yemwenso anali Mlevi. Samueli atafika, anauza Sauli kuti ufumu wake utha chifukwa sanamvere. Kenako, pamene Sauli ankatumiza gulu lake kuti likamenye nkhondo, anawalumbiritsa lumbiro losayenera. Iye anati: “Munthu aliyense wodya mkate dzuwa lisanalowe, komanso ndisanabwezere adani anga, ndi wotembereredwa.”​—1 Samueli 13:10-​14; 14:24.

Zimene Sauli analankhulazi zinasonyeza kuti akusintha ndipo anakhala munthu woipa kwambiri. Pa nthawiyi, munthu yemwe poyamba anali wodzichepetsayu anasintha kwambiri n’kukhala wodzikuza. Ndipotu Yehova sanamuuze kuti apereke lamulo loti asilikali ake, omwe anali olimba mtima komanso amphamvu, asadye chilichonse. Ndipo taganizirani mawu omwe Sauli analankhula akuti “ndisanabwezere adani anga.” Kodi mawuwa sakusonyeza kuti Sauli ankaona kuti nkhondoyo inali yake? Kapena kodi sitinganene kuti anaiwala zoti Yehova ndi amene akanamuthandiza, osati mtima wake wofuna kubwezera adaniwo kapena kufuna ulemerero komanso kutchuka koti ndi wodziwa nkhondo?

Yonatani sanadziwe chilichonse za lumbiro lomwe bambo ake anauza anthu kuti achite. Ndiyeno Yonatani atatopa chifukwa cha nkhondo yoopsayo, anatenga ndodo yake n’kupisa mu chisa cha uchi ndipo anadya. Nthawi yomweyo anapezanso mphamvu. Ndiyeno mmodzi mwa anthuwo atauza Yonatani kuti bambo ake alamula zoti anthuwo asadye chilichonse, iye anawayankha kuti: “Bambo anga achititsa kuti dziko lonse livutike. Taonani mmene maso anga ayerera chifukwa ndalawa uchi pang’ono chabe. Anthu akanadya zimene afunkha kwa adani awo, Afilisiti tikanawagonjetsa. Koma onani, sitinawakanthe mokwanira.” (1 Samueli 14:25-35) Apa Yonatani ankanena zoona. Ngakhale kuti anali mwana wokhulupirika, sankangovomereza chilichonse chimene bambo ake anena kapena kuchita. N’chifukwa chake anthu ankamulemekeza.

Sauli atamva zoti Yonatani waphwanya lamulo lomwe linakhazikitsidwa, sanaonebe kuti zimene analankhulazo zinali zopanda nzeru. M’malomwake anaona kuti ndi bwino kuti mwana wakeyo aphedwe. Yonatani sanatsutse kapena kupempha kuti amuchitire chifundo. Iye anayankha bambo akewo kuti: “Ndiphenitu.” Koma Aisiraeliwo anauza Sauli kuti: “Kodi Yonatani amene wagwira ntchito yobweretsa chipulumutso chachikulu chimenechi mu Isiraeli afe? Sizitheka zimenezo! Pali Yehova, Mulungu wamoyo, ngakhale tsitsi limodzi la m’mutu wake siligwa pansi, pakuti iye wachita zimenezi lero mothandizidwa ndi Mulungu.” Zitatero Sauli sanalankhulenso chilichonse ndipo nkhaniyo imanena kuti: “Ndi mawu amenewa anthuwo anapulumutsa Yonatani, moti sanafe.”​—1 Samueli 14:43-45.

“Ndiphenitu!”

Yonatani anali ndi mbiri yabwino chifukwa choti anali wolimba mtima, wakhama komanso analibe mtima wodzikonda. Akakumana ndi zinthu zoopsa, ankatetezedwa chifukwa cha mbiri yomwe anali nayo. Nafenso tiyenera kuonanso bwino zimene timachita tsiku lililonse kuti mbiri yathu ikhale yabwino. Paja Baibulo limanena kuti kukhala ndi mbiri yabwino ndi chinthu chamtengo wapatali. (Mlaliki 7:1) Ngati timayesetsa kukhala ndi mbiri yabwino kwa Yehova, ngati mmene zinalili ndi Yonatani, zinthu zidzatiyendera bwino kwambiri.

Mdima Wandiweyani

Ngakhale kuti Sauli ankalakwitsa zinthu zina, Yonatani sanasiye kukhalabe kumbali ya bambo akewo n’kumamenya nkhondo mokhulupirika. Koma n’zosachita kufunsa kuti Yonatani anakhumudwa kwambiri ataona kuti bambo ake ayamba mtima wodzikuza komanso wosamvera. Zinali ngati bambo akewo ali mumdima wandiweyani moti Yonatani ankalephera kuwatulutsamo.

Zinthu zinafika poipa kwambiri pamene Yehova anauza Sauli kuti akamenyane ndi Aamaleki. Mtundu wa Aamaleki unali ndi makhalidwe oipa kwambiri moti m’nthawi ya Mose, Yehova analamula kuti mtundu wonsewo uwonongedwe. (Ekisodo 17:14) Mulungu anauza Sauli kuti akawononge ziweto zawo zonse komanso akaphe Agagi mfumu yawo. Sauli anagonjetsadi adaniwo. Monga mwa nthawi zonse, n’zosakayikitsa kuti Yonatani anamvera lamulo la bambo akewo, n’kukamenya nawo nkhondoyo mwamphamvu. Koma Sauli sanamvere Yehova mwadala moti sanaphe Agagi. Sanaphenso ziweto zake zina komanso kuwononga chuma chake. Ndiyeno mneneri Samueli anapereka chiweruzo cha Yehova kwa Sauli. Iye ananena kuti: “Popeza iwe wakana mawu a Yehova, iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”​—1 Samueli 15:2, 3, 9, 10, 23.

Pasanapite nthawi izi zitachitika, Yehova anachotsa mzimu wake pa Sauli. Popeza kuti Yehova anasiya kumukonda, Sauli anakhala munthu woipa kwambiri, wa mtima wapachala komanso wochititsa mantha. Zinali ngati kuti Mulungu watumiza mzimu woipa kuti ulowe m’malo mwa mzimu wabwino womwe anali poyamba. (1 Samueli 16:14; 18:10-​12) Kodi mukuganiza kuti Yonatani anamva bwanji kuona bambo ake, omwe anali olemekezeka, akusintha n’kukhala munthu woipa? Ngakhale zinali choncho, Yonatani sanasiye kutumikira Yehova mokhulupirika. Ankathandizabe bambo akewo pa zinthu zina ndipo nthawi zina ankalankhula nawo modekha komanso mokoma mtima. Komabe Yonatani ankadalira kwambiri Yehova Mulungu, yemwe ndi Atate amene sasintha.​—1 Samueli 19:4, 5.

Kodi inuyo munaonapo munthu amene munkamukonda kwambiri, mwina wa m’banja lanu, akusintha mofulumira n’kukhala munthu woipa? Kunena zoona zimakhala zopweteka kwambiri. Zimene Yonatani anachita, zimatikumbutsa zomwe wolemba masalimo wina anadzalemba pambuyo pake. Anati: “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.” (Salimo 27:10) Tisamaiwale kuti Yehova ndi wokhulupirika. Choncho ngakhale munthu wina atakukhumudwitsani kapena kukusiyani, Mulungu adzakutengani ndipo adzakhala ngati Bambo anu.

Yonatani ayenera kuti anamva zoti Yehova akufuna kuti Sauli asakhalenso mfumu. Ndiye kodi anatani? Kapena mwina ankaganiza kuti, ‘Ngati Mulungu angandisankhe kukhala mfumu, kodi ndidzakhale mfumu yotani?’ Kodi ankaona kuti apezerapo mwayi wokonza zina ndi zina zomwe bambo ake ankalakwitsa, ndi kusonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani ya kumvera komanso kukhulupirika? Sitingadziwe zonse zomwe ankaganiza. Koma chomwe tikudziwa n’choti palibe amene ankadziwa zotsatirapo zake. Kodi pamenepa tingati Yehova anataya Yonatani, mtumiki wake wokhulupirika? Ayi ndithu. Tikutero chifukwa Yehova anagwiritsa ntchito Yonatani ngati chitsanzo chabwino kwambiri m’Baibulo, pa nkhani yokhala bwenzi lokhulupirika. M’nkhani yotsatira tidzakambirana za mmene Yonatani anasonyezera kuti ndi bwenzi lokhulupirika.