Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YONATANI

“Anagwirizana Kwambiri”

“Anagwirizana Kwambiri”

Nkhondo imene Aisiraeli ankamenyana ndi Afilisti inali itatha ndipo ku Chigwa cha Ela kunali bata. Mfumu Sauli anakumana ndi anthu ake kumisasa yawo. Kumisasayo kunali mwana wake woyamba dzina lake Yonatani ndipo mnyamata wina amene anali m’busa ankafotokoza nkhani yake mosangalala kwambiri. Mnyamatayo anali Davide ndipo anali wosangalala komanso wamtima wofuna kuchita zambiri. Sauli ankamvetsera mwachidwi kwambiri zimene Davide ankafotokoza. Koma nanga Yonatani anamva bwanji mumtima mwake? Iye anali atakhala m’gulu la asilikali a Yehova kwa nthawi yaitali ndipo anagonjetsa adani ambiri. Koma pa tsikuli Davide ndi amene anagonjetsa adani awo ngakhale kuti anali wamng’ono kwambiri. Iye anapha chiphona dzina lake Goliyati. Kodi Yonatani anachita nsanje chifukwa choti anthu ankachemerera Davide?

Mwina mungadabwe ndi zimene Yonatani anachita. Baibulo limati: “Ndiyeno Davide atangomaliza kulankhula ndi Sauli, Yonatani anagwirizana kwambiri ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.” Yonatani anafika popatsa Davide zida zake, kuphatikizapo uta wake. Mphatsoyi inali yapadera kwambiri chifukwa Yonatani anali katswiri woponya mivi. Yonatani ndi Davide anachitanso pangano loti sadzasiya kugwirizana komanso kuthandizana.—1 Samueli 18:1-5.

Umu ndi mmene mgwirizano wapadera umene unafotokozedwa m’Baibulo unayambira. Anthu a chikhulupiriro amaona kuti kukhala ndi anzawo abwino n’kofunika. Koma masiku ano anthu ambiri sakondana. Choncho tikamasankha bwino anthu ocheza nawo, kuwathandiza pa mavuto komanso kukhala okhulupirika tikhoza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. (Miyambo 27:17) Tsopano tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Yonatani pa nkhani yogwirizana ndi anthu.

Zimene Zinachititsa Kuti Azigwirizana

Kodi zinatheka bwanji kuti anthuwa ayambe kugwirizana mwamsanga chonchi? Kuti timvetse zimene zinachititsa kuti azigwirizana, tiyeni tikambirane kaye zinthu zina zokhudza Yonatani. Pa nthawiyo zinthu sizinkamuyendera bwino kwenikweni. Bambo ake ankasintha kwambiri ndipo ankangoipiraipira. Poyamba, Sauli anali munthu wodzichepetsa komanso wachikhulupiriro koma anafika pokhala mfumu yodzikuza komanso yosamvera.​—1 Samueli 15:17-​19, 26.

Zimenezi ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Yonatani chifukwa ankawakonda kwambiri bambo akewa. (1 Samueli 20:2) Mwina ankaopa kuti bambo akewo akhoza kubweretsera anthu a Yehova mavuto aakulu. Mwinanso ankaganiza kuti kusamvera kwa mfumuyo kungachititse kuti anthu ena asamamverenso ndipo Yehova angasiye kusangalala nawo. N’zosachita kufunsa kuti Yonatani, yemwe anali ndi chikhulupiriro cholimba, ankavutika kwambiri ndi zimenezi.

Zimene tafotokozazi zingatithandize kumvetsa chifukwa chake Yonatani anayamba kugwirizana ndi Davide. Iye anaona kuti Davide anali ndi chikhulupiriro cholimba. Mosiyana ndi asilikali a Sauli, Davide sankaopa Goliyati ngakhale kuti anali wamkulu kwambiri. Iye ankaona kuti kupita kunkhondo m’dzina la Yehova kungamuchititse kukhala wamphamvu kwambiri kuposa Goliyati ndi zida zake zonse.—1 Samueli 17:45-47.

Maganizo amenewa ndi amenenso Yonatani anali nawo zaka zingapo zapitazo. Iye anaona kuti ngati atapita kunkhondo anthu awiri, iyeyo ndi mtumiki wake, akhoza kukagonjetsa asilikali ambiri. Kodi chinkamulimbitsa mtima n’chiyani? Yonatani anati: “Palibe chimene chingalepheretse Yehova.” (1 Samueli 14:6) Choncho Yonatani ankafanana ndi Davide chifukwa onse ankakhulupirira kwambiri Yehova komanso kumukonda ndi mtima wonse. Zimenezi n’zimene zinachititsa kuti ayambe kugwirizana. Yonatani anali mwana wa mfumu ndipo anali atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 50, pomwe Davide anali m’busa chabe ndipo anali asanakwanitse n’komwe zaka 20. * Koma iwo sanaganizire za kusiyana kumeneku.

Pangano limene anachita linawathandiza kwambiri kuti asasiye kugwirizana. N’chifukwa chiyani tikutero? Davide ankadziwa kuti Yehova wamusankha kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli. Kodi mukuganiza kuti iye akanabisira Yonatani zimenezi? Ayi sakanamubisira. Tikutero chifukwa chakuti anthu amene amagwirizana kwambiri amauzana zoona zokhazokha ndipo sabisirana zinthu. Koma kodi Yonatani anamva bwanji atadziwa zoti Davide adzakhala mfumu? N’kutheka kuti Yonataniyo ankayembekezera kudzakhala mfumu kuti akonze zimene bambo akewo analakwitsa. Baibulo silifotokoza mmene Yonatani anamvera mumtima mwake. Limangofotokoza zinthu zofunika zokha zomwe ndi kukhulupirika komanso chikhulupiriro chake. Iye anaoneratu kuti Davide anali ndi mzimu wa Yehova. (1 Samueli 16:1, 11-13) Choncho Yonatani anachitadi zimene analonjeza ndipo ankaonabe kuti Davide ndi mnzake osati munthu wopikisana naye. Iye ankangofuna kuti zimene Yehova ankafuna zichitike.

Yonatani ndi Davide ankafanana chifukwa choti onse ankakhulupirira kwambiri Yehova komanso kumukonda ndi mtima wonse

Mgwirizano wawowu unali wothandiza kwambiri. Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Yonatani? Mtumiki wa Mulungu aliyense ayenera kuzindikira kufunika kokhala ndi anzake abwino. Anzathuwo tikhoza kusiyana nawo msinkhu kapena chikhalidwe, koma akhoza kutithandiza kwambiri ngati ali ndi chikhulupiriro cholimba. Yonatani ndi Davide ankalimbikitsana kwambiri. Zimenezi zinali zothandiza chifukwa chakuti iwo anakumana ndi mayesero ambiri.

Anayenera Kusankha Kuti Akhale Wokhulupirika kwa Ndani

Poyamba, Sauli ankakonda kwambiri Davide ndipo anamusankha kuti akhale mtsogoleri wa asilikali ake. Koma pasanapite nthawi yaitali, Sauli anachita zosiyana kwambiri ndi Yonatani. Iye anayamba kuchitira nsanje Davide. Ankachita zimenezi chifukwa Davide anapitiriza kugonjetsa Afilisti ndipo anthu ankamuchemerera komanso kumulemekeza kwambiri. Akazi ena a ku Isiraeli anafika poimba kuti: “Sauli wakantha adani ake masauzande, ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi.” Nyimbo imeneyi inkamunyansa kwambiri Sauli. Baibulo limati: “Kuyambira tsiku limenelo, Sauli anayamba kuyang’ana Davide ndi diso loipa.” (1 Samueli 18:7, 9) Iye ankaopa kuti Davide akhoza kumulanda ufumu. Koma zimenezi zinali zopusa. N’zoona kuti Davide ankadziwa kuti adzakhala mfumu yotsatira, koma sankaganiza ngakhale pang’ono zolanda ufumu kwa munthu amene Yehova anali atamudzoza.

Maulendo angapo, Sauli anakonza zoti Davide aphedwe kunkhondo, koma sizinaphule kanthu. Davide ankangopitiriza kugonjetsa adani ake ndipo anthu ankamukonda kwambiri. Kenako Sauli anakonza chiwembu china choti aphe Davide ndipo ankafuna kuti atumiki ake komanso mwana wake amuthandize. Kodi mukuganiza kuti Yonatani anamva bwanji ataona zimene bambo ake ankachitazi? (1 Samueli 18:25-30; 19:1) Yonatani anali mwana wabwino kwa bambo ake koma analinso wokhulupirika kwa Davide. Popeza Yonatani ankafuna kukhala wokhulupirika kwa onse awiriwa, kodi anatani?

Iye analimba mtima n’kuuza bambo ake kuti: “Mfumu isachimwire mtumiki wake Davide, chifukwa iye sanakuchimwireni, ndipo wakhala akukuchitirani zinthu zabwino kwambiri. Iye anaika moyo wake pangozi n’kupha Mfilisiti uja, moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu kwa Aisiraeli onse. Inuyo munaona zimenezi zikuchitika, ndipo munasangalala. Ndiye n’chifukwa chiyani mukufuna kuchimwira magazi osalakwa, mwa kupha Davide popanda chifukwa?” Atanena zimenezi, nzeru zinamubwerera Sauli ndipo analonjeza kuti sadzapha Davide. Koma Sauli sanakwaniritse zimene analonjezazi. Davide atapitiriza kupambana nkhondo, Sauli anamuchitira nsanje kwambiri moti anamuponya mkondo kuti amulase. (1 Samueli 19:4-6, 9, 10) Koma Davide anazemba n’kuthawa.

Kodi inunso pa nthawi ina munayenera kusankha kuti mukhale wokhulupirika kwa ndani? Zimenezi zimakhala zovuta kwambiri. Anthu ena angakuuzeni kuti nthawi zonse muyenera kukhala wokhulupirika kwa achibale anu. Koma Yonatani ankadziwa kuti zimenezi si zoona. Iye ankadziwa kuti si nzeru kukhala kumbali ya bambo ake m’malo mokhala kumbali ya Davide, yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Choncho Yonatani anasankha kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndipo anakhala kumbali ya Davide. N’zoona kuti ankaona kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova n’kofunika kwambiri, koma anakhalanso wokhulupirika kwa bambo ake. Tikutero chifukwa chakuti anawalangiza mosapita m’mbali m’malo mongowauza zimene zikanawasangalatsa. Tonsefe tingachite bwino kutsanzira Yonatani pa nkhani yokhala wokhulupirika.

Anavutika Chifukwa Chokhala Wokhulupirika

Yonatani anayesetsa kuthandiza Sauli kuti ayambe kugwirizana ndi Davide koma sizinatheke. Davide anazemba n’kupita kwa Yonatani kukamuuza kuti akuopa kuti aphedwa. Iye anauza mnzakeyo kuti: “Imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!” Yonatani anavomera kuchita zinthu zina kuti adziwe maganizo a bambo ake pa nkhaniyi kenako n’kudziwitsa Davide. Anauza Davide kuti abisale penapake ndipo iye adzamupatse chizindikiro pogwiritsa ntchito uta ndi mivi. Yonatani anapempha Davide kuti alonjeze chinthu chimodzi. Iye anamuuza kuti: “Chonde, usadzasiye kusonyeza nyumba yanga kukoma mtima kosatha mpaka kalekale. Ngakhalenso pamene Yehova adzawononga mdani aliyense wa Davide padziko lapansi.” Davide analonjeza kuti adzasamalira komanso kuteteza anthu a m’banja la Yonatani.—1 Samueli 20:3, 13-27.

Yonatani anayesa kuuza Sauli zinthu zabwino zokhudza Davide koma anakwiya kwambiri. Anafika ponena kuti Yonataniyo anali “chimwana cha mkazi wopanduka.” Ananenanso kuti zimene ankachitira Davide n’zochititsa manyazi banja lake lonse. Kenako anafuna kuti Yonataniyo ayambe mtima wodzikonda pomuuza kuti: “Masiku onse amene mwana wa Jeseyo adzakhala ndi moyo, iweyo ndi ufumu wako sudzakhazikika ayi.” Koma Yonatani sanasinthe maganizo ake ndipo anawafunsa bambo akewo kuti: “Aphedwe chifukwa chiyani? Walakwanji?” Sauli anapsa mtima kwambiri. Ngakhale kuti anali wachikulire, iye anali adakali msilikali wamphamvu. Ndipo anaponya mkondo kuti alase mwana wakeyo. Koma ngakhale kuti anali katswiri, anamuphonya. Zimenezi zinamupweteka kwambiri Yonatani komanso kumuchititsa manyazi ndipo anangochokapo.—1 Samueli 20:24-​34.

Yonatani anasonyeza kuti sanali wodzikonda

Kutacha, Yonatani anapita kutchire pafupi ndi malo amene Davide anabisala. Malinga ndi zimene anagwirizana, iye anaponya muvi kuti adziwitse Davide zoti Sauli akufunabe kumupha. Kenako anauza mtumiki wake kuti abwerere kumzinda. Apa tsopano Yonatani ndi Davide anatsala awiriwiri ndipo anali ndi kampata kocheza. Onse analira kenako Yonatani anatsanzikana ndi Davide, yemwe anayamba moyo wothawathawa.—1 Samueli 20:35-42.

Yonatani anasonyeza kuti anali wokhulupirika osati wodzikonda. Satana, yemwe ndi mdani wa anthu onse okhulupirika, akanakonda kuona Yonatani akutengera bambo ake n’kumaganizira kwambiri za udindo komanso ulemerero wake. Paja Satana amatinyengerera kuti tizikhala odzikonda. Iye anakwanitsa kuchita zimenezi kwa Adamu ndi Hava. (Genesis 3:1-6) Koma analephera kupusitsa Yonatani ndipo ayenera kuti anakwiya kwambiri. Kodi inunso mudzapewa kupusitsidwa ndi Satana? Masiku ano anthu ambiri ndi odzikonda. (2 Timoteyo 3:1-5) Kodi tidzatsanzira Yonatani pa nkhani yokhala okhulupirika komanso osadzikonda?

Yonatani anali wokhulupirika kwa Davide ndipo anamupatsa chizindikiro chomuthandiza kuti asaphedwe

“Unali Wosangalatsa Kwambiri kwa Ine”

Sauli anafika pomangoganizira zopha Davide basi. Palibe zimene Yonatani akanachita pamene bambo ake ankatenga asilikali ambirimbiri n’kumakasakasaka Davide kuti amuphe ngakhale kuti sanalakwe chilichonse. (1 Samueli 24:1, 2, 12-15; 26:20) Kodi Yonatani anatani? Malemba sasonyeza kuti Yonatani anali ndi bambo akewo pamene ankapita kukasakasaka Davide. Yonatani sakanachita zimenezo chifukwa ankafuna kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndi Davide komanso kukwaniritsa lonjezo lake lija.

Yonatani sanasiye kukonda mnzakeyo moti anapeza njira yoti akakumanenso naye. Ndipo anakakumana naye ku Horesi, dzina limene limatanthauza kuti “Nkhalango.” Dera limeneli linali la mapiri okhala ndi nkhalango ndipo linali pa mtunda wa makilomita ochepa kum’mwera chakum’mawa kwa Hebroni. N’chifukwa chiyani Yonatani analolera kuika moyo wake pa ngozi kuti akaone Davide? Baibulo limanena kuti anali ndi cholinga choti “akalimbikitse Davide kudalira Mulungu.” (1 Samueli 23:16) Ndiye kodi anamulimbikitsa bwanji?

Yonatani anauza mnzakeyo kuti: “Usachite mantha.” Kenako anamutsimikizira kuti: “Dzanja la Sauli bambo anga silikupeza.” Yonatani anatha kumutsimikizira zimenezi chifukwa chokhulupirira kwambiri kuti cholinga cha Yehova sichingalephereke. Kenako ananena kuti: “Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli.” Mneneri Samueli anali atanena zomwezo zaka zambiri zapitazo ndipo pa nthawiyi Yonatani ankakumbutsa Davide kuti nthawi zonse mawu a Yehova amakwaniritsidwa. Nanga Yonatani ankaona kuti udindo wake udzakhala wotani? Iye anauza Davide kuti: “Ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.” Apa anasonyezatu kudzichepetsa kwambiri. Anasonyeza kuti sangadandaule kutumikira munthu wamng’ono kwa iye, yemwe ankasiyana naye zaka 30. Pomaliza Yonatani anati: “Sauli bambo anga akudziwa bwino zimenezi.” (1 Samueli 23:17, 18) Pansi pa mtima, Sauli ankadziwa kuti n’zosatheka kuti awine polimbana ndi munthu amene Yehova anamusankha kuti adzakhale mfumu.

Yonatani analimbikitsa Davide pamene ankavutika

Pa zaka zotsatira, Davide ayenera kuti ankakumbukira komanso kulimbikitsidwa ndi mawu amene Yonatani anamuuzawa. Aka kanali komaliza kuti akumane. N’zomvetsa chisoni kuti zimene Yonatani ankayembekezera, zoti adzakhale wachiwiri kwa Davide, sizinatheke.

Yonatani anapita kunkhondo limodzi ndi bambo ake kuti akamenyane ndi Afilisti, omwe anali adani a Aisiraeli. Ngakhale kuti bambo ake ankalakwitsa zinthu zambiri, Yonatani anakamenya nawo nkhondoyo. Anachita zimenezi chifukwa choona kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri. Iye anamenya nkhondoyo molimba mtima komanso mokhulupirika ngati mmene ankachitira nthawi zonse koma Aisiraeli sizinawayendere bwino. Sauli anafika pochita zoipa kwambiri moti anayamba kukhulupirira mizimu. Limeneli linali tchimo lalikulu m’Chilamulo cha Mulungu choncho Yehova anasiya kumudalitsa. Yonatani ndi ana ena awiri a Sauli anaphedwa pa nkhondoyo. Ndipo Sauli anavulazidwa kenako n’kudzipha.—1 Samueli 28:6-14; 31:2-6.

Yonatani ananena kuti: “Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.”—1 Samueli 23:17.

Davide atamva zimenezi analira kwambiri. Iye anali munthu wachifundo moti analiriranso Sauli ngakhale kuti Sauliyo anamuzunza kwambiri. Davide analemba nyimbo yodandaula chifukwa cha imfa ya Sauli ndi Yonatani. Koma mawu ogwira mtima kwambiri amene analemba m’nyimboyi anali okhudza Yonatani. Iye ananena kuti: “Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe m’bale wanga Yonatani, unali wosangalatsa kwambiri kwa ine. Chikondi chako chinali chapamwamba kwambiri kuposa chikondi cha akazi.”—2 Samueli 1:26.

Davide sanaiwale zimene analonjeza Yonatani. Patapita zaka zambiri, iye anafufuza mwana wa Yonatani amene anali wolumala dzina lake Mefiboseti n’kuyamba kumusamalira. (2 Samueli 9:1-13) Apa zikuonekeratu kuti Davide anaphunzira zambiri kwa Yonatani pa nkhani yokhala wokhulupirika kwa mnzake ngakhale zinthu zitavuta. Kodi ifenso tingatsanzire Yonatani pa nkhani imeneyi? Nanga tingapeze anzathu abwino ngati Yonatani? Kodi tingatsanzire Yonatani pa nkhani yothandiza anzathu? Tikhoza kufanana ndi Yonatani komanso kutsanzira chikhulupiriro chake. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kuthandiza anzathu kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Tizionanso kuti kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi kofunika kwambiri komanso tizikhala okhulupirika kwa ena m’malo mokhala odzikonda.

^ ndime 10 Yonatani amatchulidwa koyamba m’Malemba chakumayambiriro kwa ulamuliro wa Sauli ndipo anali mtsogoleri wa asilikali. Choncho pa nthawiyo ayenera kuti anali atakwanitsa zaka 20. (Numeri 1:3; 1 Samueli 13:2) Sauli analamulira kwa zaka 40. Choncho pamene Sauliyo ankamwalira ndiye kuti Yonatani ali ndi zaka za m’ma 60. Koma Davide anali ndi zaka 30 pamene Sauli ankamwalira. (1 Samueli 31:2; 2 Samueli 5:4) Choncho Yonatani ayenera kuti ankasiyana ndi Davide zaka 30.