Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Ana ndi Mafoni—Mbali Yoyamba: Kodi Mwana Wanga Akhale ndi Foni?

Ana ndi Mafoni—Mbali Yoyamba: Kodi Mwana Wanga Akhale ndi Foni?

 Ana ambiri masiku ano ali ndi foni, a ndipo ambiri amalowa pa intaneti ndi foniyo ali okhaokha kuchipinda kwawo. Kodi kulola mwana wanu kukhala ndi foni kungabweretse mavuto anji? Nanga kuli ndi ubwino wanji? Kodi mwana wanu ayenera kukhala pafoni nthawi yochuluka bwanji tsiku lililonse?

 Zimene muyenera kudziwa

 Ubwino Wake

 •   Amateteza ana, amakhazika mtima pansi makolo. “Tikukhala m’dziko loopsa,” anatero a Bethany, omwe ali ndi ana awiri azaka zapakati pa 13 ndi 19. “M’pofunika kwambiri kuti ana azitha kulumikizana ndi makolo awo.”

   Mayi ena dzina lawo a Catherine ananenanso kuti, “Pali mapulogalamu ena omwe kholo lingathe kugwiritsira ntchito kuti lilumikizane ndi foni ya mwana wake kuti lione komwe mwanayo ali. Ngati mwanayo akuyendetsa galimoto, khololo likhoza kuona kuti akuthamanga kwambiri bwanji.”

 •   Amathandiza kusukulu. Mayi ena dzina lawo a Marie anati: “Ana amalandira homuweki pa imelo kapena pa mauthenga apafoni, ndipo amagwiritsa ntchito njira zomwezo polankhulana ndi aphunzitsi awo.”.

 Kuipa Kwake

 •   Kukhala nthawi yaitali pafoni. Achinyamata ambiri amakhala maola ambiri ali pafoni tsiku lililonse. Ndipo nthawi imene makolo ambiri amathera pafoni sisiyana ndi imene amakhala akulankhula ndi ana awo. Mlangizi wina anati mabanja ambiri masiku ano amakhala ngati “alendo amene amakumana lipamodzi tsiku lillonse koma salankhulana chifukwa aliyense maso amakhala ali pafoni.” b

 •   Kuonera zinthu zolaula. Malinga ndi kafukufuku wina, achinyamata oposa hafu amachita kusakasaka zithunzi zolaula mwezi uliwonse. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa kuonera zinthu zolaula masiku ano n’kosavuta pafoni. A William, omwe ali ndi ana awiri azaka zapakati pa 13 ndi 19 anati: “Kholo likapatsa mwana foni, limakhala ngati lamupatsa shopu yoonetsa zithunzi zolaula yoti aziyenda nayo kulikonse.”

 •   Kusafuna kuisiya pansi. Anthu ambiri satha kuisiya pansi foni yawo. Akapanda kudziwa komwe ili, amayamba kupumira m’mwamba, kuda nkhawa, ngakhale kudwala kumene. Makolo ena amaona kuti ana awo amachita mwano akakhala pafoni. “Nthawi zina ndikafuna kulankhula ndi mwana wanga, amandiyang’ana moipidwa kapena kuyankha zamwano chifukwa safuna kuti ndimusokoneze,” anatero a Carmen.

 •   Kuopsa kwina. Mwana akamagwiritsa ntchito foni pa intaneti, akhozanso kumaopsezedwa ndi anzake kapena kumatumiziridwa mameseji okhudza zogonana. Komanso akhoza kudwala matenda ena chifukwa chokhala mopindika nthawi zonse ndiponso chifukwa chosagona mokwanira. Posafuna kuti makolo awo adziwe zimene zili pafoni pawo, achinyamata ena amagwiritsa ntchito mapulogalamu a pafoni amene amaoneka ngati abwinobwino, mwachitsanzo ooneka ngati kakyuleta, pofuna kubisa mapulogalamu oipa.

   A Daniel, omwe ali ndi mwana wamkazi wazaka zapakati pa 13 ndi 19, anafotokoza bwino vuto limeneli. Iwo anati: “Foni imapatsa munthu mwayi wotha kuona chilichonse chimene chili pa intaneti, kaya chabwino kapena choipa.”

 Zimene muyenera kudzifunsa

 •   ‘Kodi mwana wanga akufunikadi kukhala ndi foni yotha kulowa pa intaneti?’

   Baibulo limati: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Poganizira mfundo imeneyi, dzifunseni kuti:

   “Kodi mwana wanga akufunika kukhala ndi foni kuti akhale wotetezeka komanso pa zifukwa zina? Kodi ndaganizira mofatsa ubwino wake komanso kuipa kwake? Kodi angathe kugwiritsa ntchito foni yamtundu wina kapena chipangizo china?”

   Bambo wina dzina lake Todd anati: “Mafoni opanda intaneti alipobe, ndipo angakuthandizeni kuti muzilankhulana ndi mwana wanu kapena kumutumizira mameseji. Angakuthandizeninso kuti musamawononge ndalama zambiri.”

 •   ‘Kodi mwana wanga ndi wokonzeka kukhala ndi udindo umenewu?’

   Baibulo limati: “Mtima wa munthu wanzeru uli kudzanja lake lamanja,” kapena kuti, umamutsogolera kunjira yoyenera. (Mlaliki 10:2) Poganizira mfundo imeneyi, dzifunseni kuti:

   ‘Kodi pali zifukwa zotani zimene zikundipangitsa kuganiza kuti ndikhoza kumukhulupirira mwana wanga? Kodi panopa timalankhulana momasuka? Kodi mwana wanga amandibisira zinthu nthawi zina? Machitsanzo, kodi amandibisira anthu amene amacheza nawo? Kodi amadziletsa pogwiritsa ntchito zipangizo zina monga TV, tabuleti, kapena kompyuta?’ Mayi ena dzina lawo a Serena anati: “Foni ndi chida chothandiza kwambiri, komanso choopsa. Muyenera kuganizira mofatsa udindo umene mukupatsa mwana wanu, popeza ndi munthu woti sanakhwime maganizo.”

 •   ‘Kodi ineyo ndine wokonzeka kukhala ndi udindo umenewu?

   Baibulo limati: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera.” (Miyambo 22:6) Poganizira mfundo imeneyi, dzifunseni kuti:

   ‘Kodi ndikuidziwa mokwanira foniyo moti ndingathe kufotokozera mwana wanga kuopsa kwake komanso mmene angadzitetezere? Kodi ndimatha kugwiritsa ntchito mapulogalamu apafonipo amene amathandiza makolo kuchepetsa zimene mwana angathe kuchita ndi foniyo? Kodi ndimuthandiza bwanji mwana wanga kugwiritsa ntchito foniyo mosamala?’ A Daniel, omwe tinawagwira mawu koyambirira aja, anati: “N’zomvetsa chisoni kuti makolo ambiri amangom’patsa mwana foni, basi n’kusiyira pompo osakhala nazonso ntchito.”

 Mfundo yofunika kwambiri: Ana amafunika kuphunzitsidwa kugwiritsa ntchito foni moyenera. Buku lina linati: “N’zosavuta kuti mwana ayambe kuthera nthawi yochuluka kwambiri pamafoni ndi zipangizo zina, makamaka ngati makolo ake sanamupatse malangizo alionse a momwe ayenera kuzigwiritsira ntchito komanso ngati iwo sadziwa zimene mwanayo amachita pafonipo.”-Indistractable.

a Munkhani ino tikunena za foni yotha kulowa pa intaneti.

b Kuchokera m’buku lakuti Disconnected, lolembedwa ndi Thomas Kersting.