Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mungathandize Bwanji Mwana Wanu Kuti Azikhoza Bwino Kusukulu?

Mungathandize Bwanji Mwana Wanu Kuti Azikhoza Bwino Kusukulu?

Zikuoneka kuti mwana wanu alibe chidwi ndi sukulu. Akapatsidwa homuweki, salemba ndiponso sakonda kuwerenga. Panopa sakukhozanso bwino komanso khalidwe lake lasinthiratu. Ndiye kodi mungamuthandize bwanji kuti azikhoza bwino kusukulu?

 Zimene muyenera kudziwa

Mukamapanikiza mwana wanu vutoli limakula. Mwana wanu akamapanikizika, amayamba kukhala ndi nkhawa akakhala kusukulu ndiponso kunyumba. Poopa kum’panikiza ndi mafunso angayambe kunama, kubisa mmene wakhozera, kulemba zabodza pa lipoti lake la kusukulu mwinanso kungosiyiratu sukulu. Zikafika pamenepa vutolo limangokulirakulira.

Vuto lomwe lingakhalepo mukamamupatsa mphatso. Bambo wina dzina lake Andrew ananena kuti: “Mwana wathu akakhoza bwino, tinkamupatsa mphatso. Zimenezi zinachititsa kuti maganizo ake onse azingokhala pa mphatsoyo. Zikakhala kuti sanakhoze bwino kwenikweni, ankakhumudwa kwambiri osati chifukwa choti sanakhoze, koma podziwa kuti salandira mphatso.”

Musamaimbe mlandu aphunzitsi ake. Mukamachita zimenezi, mwana wanu sangazindikire kuti kukhoza bwino kumafuna kulimbikira. Angayambenso kumaloza ena chala pa zinthu zoti walakwitsa ndi iyeyo n’kumayembekezera kuti wina akonza zolakwikazo. Mwachidule tingati, sangaphunzire kuvomereza akalakwitsa. Mwana wanu akamavomereza zomwe walakwitsa, zidzamuthandiza akadzakula.

 Zimene mungachite

Muziugwira mtima. Ngati mwakhumudwa ndi zinazake, musamakambirane ndi mwana wanuyo zokhudza sukulu mpaka mutapeza nthawi ina yabwino. Bambo wina dzina lake Brett ananena kuti: “Ine ndi mkazi wanga timaona kuti zimayenda bwino kukambirana ndi ana athu za mmene akhozera kusukulu, mitima yathu ikakhala m’malo.”

Lemba lothandiza: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.”​—Yakobo 1:19.

Pezani chomwe chikuchititsa. Nthawi zambiri ana amalakwa kusukulu chifukwa chovutitsidwa ndi anzawo, kusinthasintha masukulu komanso kuchita mantha ndi mayeso. Nthawi zina mavuto a kunyumba, kusagona mokwanira, kusawerenga kapenanso kupanda chidwi ndi sukulu, zingachititsenso kuti azilakwa. Choncho musamathamangire kuganiza kuti mwanayo ndi waulesi.

Lemba lothandiza: “Munthu wosonyeza kuzindikira pa zinthu adzapeza zabwino.”​—Miyambo 16:20.

Muzimuthandiza. Mukonzeretu nthawi yoti azilemba homuweki komanso kuwerenga. Mungamukonzere malo abwino kuti asasokonezeke ndi chilichonse, kaya TV kapena foni. Kuti asamasokonezeke polemba homuweki, muziduladula nthawiyo ndi kum’patsa mpata wopuma n’kudzapitiriza homuwekiyo kanthawi kena. Bambo wina wa ku Germany dzina lake Hector ananena kuti: “Mayeso akamayandikira, tsiku lililonse timapatulako ka nthawi kobwereza ndi mwana wathuyo zomwe wakhala akuphunzira.”

Lemba lothandiza: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.”​—Mlaliki 3:1.

Muzimuuza ubwino wa maphunziro. Mwana wanu akamvetsa ubwino wa sukulu panopa, zingamuthandize kuti azilimbikira. Mwachitsanzo, mungamuuze kuti phunziro la masamu, lingamuthandize kuti azitha kukonza bajeti pa ndalama zomwe mumamupatsa.

Lemba lothandiza: “Upeze nzeru, upezenso luso lomvetsa zinthu. . . . Uzilemekeze kwambiri.”​Miyambo 4:5, 8.

Zimene zingakuthandizeni: Muzithandiza mwana wanu kulemba homuweki, koma musamamulembere. A Andrew ananena kuti: “Mwana wathu ankangodalira ifeyo, m’malo moti aziganiza yekha kuti apeze mayankho.” Choncho muzimuthandiza kudziwa mmene angalembere homuweki payekha.