Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingakwanitse Kukakhala Pandekha?

Kodi Ndingakwanitse Kukakhala Pandekha?

Kuyambira pachiyambi, Mulungu anafuna kuti achinyamata akakula azisiya makolo awo n’kukayamba banja lawo. (Genesis 2:23, 24; Maliko 10:7, 8) Koma kodi mungadziwe bwanji kuti mwakonzeka kuchoka pakhomo pa makolo anu? Taganizirani mafunso atatu ofunika awa.

 Kodi ndikufuna kuchoka chifukwa chiyani?

Taganizirani zifukwa zotsatirazi. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi zifukwa zikuluzikulu ziti zimene zikundichititsa kuti ndichoke pakhomo pa makolo anga?’

  • Kuthawa mavuto a panyumba

  • Ndikufuna ufulu wochita zimene ndikufuna

  • Ndikufuna anzanga azindilemekeza

  • Ndikufuna kukakhala ndi mnzanga amene akusowa munthu wokhala naye

  • Ndikufuna kukagwira ntchito yongodzipereka kwinakwake

  • Ndikufuna kuphunzira kukhala pandekha

  • Makolo anga apume kundisamalira

  • Zifukwa zina

Zifukwa zimene zatchulidwazi pazokha sikuti ndi zoipa. Komabe funso ndi lakuti, Kodi mukufuna kuchoka pakhomo pa makolo anu chifukwa chiyani? Mwachitsanzo, ngati mukuchoka chifukwa chongofuna kukhala ndi ufulu wochita zofuna zanu, mungakadabwe kuti zimene mumayembekezera si zimene zikuchitika.

Danielle, yemwe anachoka pakhomo pa makolo ake kwa kanthawi ali ndi zaka 20, anaphunzira zambiri pa zimene anakumana nazo atachoka. Iye anati: “Ngakhale utakhala wekha, sungakwanitse kuchita chilichonse chimene ukufuna chifukwa cha kuchuluka kwa ntchito komanso mavuto a ndalama.” Choncho, musalole kuti winawake akuumirizeni kuchita zinthu mopupuluma, monga kuchoka panyumba ya makolo anu.Miyambo 29:20.

 Kodi ndine wokonzeka kuchoka?

Kuchoka pakhomo pa makolo anu kuli ngati kuyamba ulendo wopita kunkhalango. Muyenera kuphunzira zinthu zina zofunika musanayambe ulendo umenewu

Kuchoka pakhomo pa makolo anu kuli ngati kuyamba ulendo wopita kunkhalango muli nokhanokha. Kodi mungayambe ulendo umenewu musakudziwa kusonkha moto, kuphika zakudya, kapena kugwiritsa ntchito mapu? Ayi. Komabe achinyamata ambiri amachoka pakhomo pa makolo awo asanaphunzire zinthu zambiri zofunika kuti munthu akhale payekha.

Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Kuti mudziwe ngati muli wokonzeka kuchoka pakhomo pa makolo anu, taganizirani zotsatirazi:

Kusamala ndalama. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Serena, anati: “Chibadwireni sindinagulepo kanthu ndi ndalama zanga. Choncho ndimaopa kuchoka pakhomo pa makolo chifukwa ndimaona kuti sindingathe kudzilipirira zinthu zofunika pa moyo wanga komanso sindingathe kusamala ndalama.” Kodi inuyo mungatani kuti muphunzire kusamala ndalama?

Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.” (Miyambo 1:5) Choncho mungachite bwino kufunsa makolo anu kuti akuuzeni ndalama zimene munthu mmodzi angawononge mwezi uliwonse polipira lendi, kugula chakudya, ndiponso kusamala galimoto kapena kulipira basi. Kenako pemphani makolo anuwo kuti akuphunzitseni kulemba bajeti ndi kulipira mabilu.

Ntchito zapakhomo. Mnyamata wina wazaka 17, dzina lake Brian, ananena kuti chimene amaopa kwambiri akaganizira zochoka pakhomo pa makolo ake n’chakuti azikachapa yekha zovala. Kodi mungadziwe bwanji kuti mwakonzeka kukadzisamalira nokha? Mnyamata winanso dzina lake Aron, yemwe ali ndi zaka 20, anafotokoza zinthu zomwe zingakuthandizeni kudziwa ngati mwakonzeka. Iye anati: “Kwa mlungu umodzi, yesani kudzichitira chilichonse ngati kuti mukukhala nokha. Muziphika nokha chakudya, muzikagula nokha zinthu kumsika komanso muzigwiritsa ntchito ndalama zanu. Muzichapa ndi kusita nokha zovala. Muzisesa ndi kukolopa nokha m’nyumba. Ndipo mukafuna kupita ku ulendo winawake, muzipita nokha popanda wina kukakusiyani kapena kukakutengani pa galimoto.” Kutsatira malangizo amenewa kungakuthandizeni m’njira ziwiri izi: (1) Mungaphunzire kugwira ntchito ndiponso (2) mungayambe kuyamikira kwambiri zimene makolo anu amakuchitirani.

Kukhala bwino ndi anthu. Kodi mumagwirizana ndi makolo komanso abale anu? Ngati simugwirizana nawo, n’zovuta kukagwirizana ndi mnzanu amene mukufuna kukakhala naye. Taganizirani zimene mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Eve, ananena. Iye anati: “Anzanga ena awiri ankagwirizana kwambiri, koma atayamba kukhala limodzi anaona kuti sangakwanitse kukhalira limodzi. Iwo anali osiyana kwambiri chifukwa wina anali waukhondo pamene wina anali wauve. Wina anali wokonda Mulungu, pamene wina sankakonda Mulungu kwenikweni. Choncho, zinthu sizinkayenda.”

Kodi munthu angatani kuti athane ndi vuto limeneli? Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Erin, anati: “Munthu angaphunzire zambiri zokhudza mmene angakhalire ndi anthu pamene ali pakhomo pa makolo ake. Angaphunzire mmene angathetsere mavuto komanso kukhala ndi mtima wololera. Ndazindikira kuti anthu amene amathawa pakhomo pa makolo awo pofuna kupewa kukangana, saphunzira kuthetsa kusamvana. Iwo amangophunzira kuthawa mavuto.”

Kulambira Mulungu ndiponso kuwerenga Baibulo. Ena amachoka pakhomo pa makolo awo kuti apewe kuchita nawo zinthu zimene makolowo amakonda, monga kulambira Mulungu komanso kuwerenga Baibulo. Ena akachoka amakapitirizabe kuphunzira Baibulo ndiponso kulambira Mulungu, koma pakangopita nthawi yochepa amasiya n’kuyamba kuchita zinthu zoipa. Kodi mungatani kuti ‘chikhulupiriro chanu chisasweke ngati ngalawa’?1 Timoteyo 1:19.

Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo, sankhani masiku ena amene mukufuna kuti muziphunzira Baibulolo mozama ndipo muzichitadi zimenezo pamasiku amenewo. Mungalembe pakalendala masikuwo, n’kuyesetsa kuchita zimenezo kwa mwezi umodzi popanda kuchita kuuzidwa ndi makolo anu.

 Kodi ndikulowera kuti?

Kodi mukufuna kuchoka pakhomo pa makolo anu kuti muthawe mavuto kapena chifukwa simukufuna kuti makolo anu azikuuzani zochita? Ngati zili choncho, ndiye kuti mukungoganizira za mavuto amene mukuwathawa osati za mavuto amene mungakakumane nawo. Koma kuchita zimenezi n’chimodzimodzi ndi munthu woyendetsa galimoto amene akungoyang’ana kumene akuchokera osati kumene akupita. Munthu wochita zimenezo, akhoza kuchita ngozi chifukwa sangaone zimene zili kutsogolo. Choncho, kuti zinthu zikuyendereni bwino, musangoganizira zochoka pakhomo pa makolo anu koma muziganiziranso za zimene mukachite mukachoka.

Kaya mukufuna kuchoka pakhomo pa makolo anu pa zifukwa zotani, koma muyenera kuganizira nkhaniyi mofatsa. Baibulo limati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Muyeneranso kumvera malangizo a makolo anu. (Miyambo 23:22) Mungachite bwino kupemphera kuti Mulungu akupatseni nzeru. Komanso ganizirani mfundo za m’Baibulo zimene takambirana m’nkhaniyi.

Choncho mukamaganizira funso lakuti, Kodi ndingakwanitse kukakhala pandekha?, muziganiziranso funso lofunika kwambiri lakuti, Kodi ndingakwanitse kuchita zinthu zonse zimene munthu amafunika kuchita akamakhala payekha? Ngati mungayankhe kuti inde, ndiye kuti ndinu okonzeka kukakhala panokha.