Pitani ku nkhani yake

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Yehova Anapulumutsa Aisiraeli

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene Yehova anapulumutsira Aisiraeli akuthamangitsidwa ndi asilikali a ku Iguputo kenako Aisiraeliwo n’kutsekerezedwa ndi Nyanja Yofiira. Werengani nkhaniyi pawebusaitiyi kapena patsamba limene mwasindikiza.

Danieli Anamvera Yehova

Danieli anatengedwa n’kupita kutali ndi banja lake. Kodi akanatha kupitiriza kumvera Yehova ndi mmene zinalirimu?

Yehova Anathandiza Solomo Kuti Akhale Wanzeru

Mfumu Solomo anali wanzeru kwambiri kuposa mfumu ina iliyonse pa dziko lapansi. Kodi Solomo anakhala bwanji ndi nzeru? Ndi zinthu ziti zimene analakwitsa pambuyo pake?

Yehova Amakhululuka ndi Mtima Wonse

Mfumu Manase inkachita zamatsenga, inkalambira milungu yabodza, ndiponso inkapha anthu osalakwa. Komabe Yehova anali wofunitsitsa kuikhululukira. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chani pa nkhani yokhululuka?