Pitani ku nkhani yake

ZITHUNZI ZOFOTOKOZA NKHANI ZA M’BAIBULO

Nowa Ankakhulupirira Kwambiri Mulungu

Phunzirani za Nowa yemwe anamanga chingalawa chachikulu n’cholinga choti apulumutse banja lake ndi nyama. Werengani nkhaniyi pa intaneti kapena sindikizani PDF yake.

Danieli Anamvera Yehova

Danieli anatengedwa n’kupita kutali ndi banja lake. Kodi akanatha kupitiriza kumvera Yehova ndi mmene zinalirimu?

Yehova Anathandiza Solomo Kuti Akhale Wanzeru

Mfumu Solomo anali wanzeru kwambiri kuposa mfumu ina iliyonse pa dziko lapansi. Kodi Solomo anakhala bwanji ndi nzeru? Ndi zinthu ziti zimene analakwitsa pambuyo pake?

Yehova Amakhululuka ndi Mtima Wonse

Mfumu Manase inkachita zamatsenga, inkalambira milungu yabodza, ndiponso inkapha anthu osalakwa. Komabe Yehova anali wofunitsitsa kuikhululukira. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chani pa nkhani yokhululuka?