Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

ZOTI MUCHITE POPHUNZIRA BAIBULO

ZOTI MUCHITE POPHUNZIRA BAIBULO

Muzilandira Uphungu Modzichepetsa

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Davide anachita polapa tchimo limene anachita ndi Bati-seba, komanso chifukwa chake Yehova anamukhululukira. Koperani nkhani ya m’Baibuloyi, iwerengeni, ndipo muiganizire mozama n’kuona mmene ingakuthandizireni.

Pirirani Mavuto Mosangalala

Onani zimene zinathandiza Paulo ndi Sila kuti azisangalalabe ngakhale kuti ankazunzidwa.

Pewani Kulakalaka Zinthu Zoipa

Chitani zimene mwauzidwa kuti muchite, ndipo mukamawerenga nkhani ya m’Baibuloyi ya Davide ndi Bati-seba, muziyerekezera kuti mukuona zimene zikuchitikazo. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhaniyi?

Pewani Mtima Wodzikuza

Abisalomu, yemwe anali mwana wa Mfumu Davide, ankafuna kulanda ufumu wa bambo ake. Koma mtima wake wodzikuzawu unam’chititsa kuti ataye moyo wake.