Pitani ku nkhani yake

Zimene Achinyamata Anzanu Amanena

Onerani mavidiyo a achinyamata a m’mayiko osiyanasiyana akufotokoza mavuto amene amakumana nawo komanso zimene amachita pothana ndi mavutowo.

 

Kuwerenga Baibulo

Kuwerenga sikophweka, koma kuwerenga Baibulo n’kothandiza kwambiri. Achinyamata anayi akufotokoza mmene kuwerenga Baibulo kwawathandizira.

Kukhulupirira Kuti Kuli Mulungu

M’vidiyo ya maminitsi atatuyi, achinyamata akufotokoza chifukwa chake amakhulupirira kuti kuli Mulungu.

Moyo Wabwino Kwambiri

Kodi mukufuna kukhala munthu wosangalala? Mvetserani pamene Cameron akufotokoza zimene zinamuthandiza kuti akhale wosangalala atapita kumalo amene samaganizira kuti angafikeko.

Maonekedwe

N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri zimawavuta kuti azisangalala ndi mmene amaonekera? N’chiyani chingawathandize pa nkhaniyi?

Nkhanza Zokhudza Kugonana

Onani zimene achinyamata 5 ananena pa nkhani yochitiridwa nkhanza zokhudza kugonana komanso zimene mungachite wina akakuchitirani nkhanzazo.