Pitani ku nkhani yake

Mavidiyo Amakatuni

Timavidiyo timeneti timaphunzitsa mfundo zofunika kwambiri koma timapangitsa kuti kuphunzirako kuzikhala kosangalatsa

 

Kodi Mumakonda Kusewera Magemu a Pakompyuta?

Kusewera magemu a pakompyuta kungakhale kosangalatsa koma kulinso ndi mavuto ake. Kodi mungatani kuti mupewe mavuto ake n’kumachita zinthu zopindulitsadi?

Zimene Mungachite Kuti Muyambirenso Kusangalala

Kodi mungatani ngati mukukhalabe okhumudwa kwa nthawi yaitali?

Zimene Muyenera Kudziwa pa Nkhani Yochita Masewera

Masewera angakuthandizeni kukhala ndi maluso enaake, monga kuchita zinthu mogwirizana ndi anthu ena. Kodi masewera muyenera kuwaika m’gulu la zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu?

Ganizirani Zimene Zingachitike Ngati Mutamwa Mowa

Kuchita zinthu chifukwa cha mowa, anthu ambiri amanena kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake amanong’oneza nazo bondo. Kodi mungatani kuti mupewe mavuto amene amakhalapo chifukwa chomwa kwambiri mowa?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?

Kodi mungatani kuti mulankhulane ndi makolo anu pamene mukuona ngati simufuna kulankhula?

Kodi Zipangizo Zanu Zimakulamulirani Kapena Mumazilamulira?

Masiku ano anthu ambiri akugwiritsa ntchito zipangizo zamakono, koma musamalole kuti zimenezi zizilamulira moyo wanu. Nanga mungadziwe bwanji kuti mwayamba kukonda kwambiri zipangizo zanu? Ngati mulidi ndi vuto limeneli kodi mungatani kuti mulithetse?

Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindilolako Kuchita Zinthu Zina?

Mukhoza kuganiza kuti makolo anu akuyenera kumakuonani kuti ndinu munthu wamkulu, koma iwo sangagwirizane ndi maganizo amenewa. Kodi mungachite zinthu ziti kuti makolo anu ayambe kukukhulupirirani?

Kodi Ndingatani Kuti Ndithetse Miseche?

Ngati anzanu ayamba kulankhula zonyoza kapena zoipa za anthu ena, musayankhire nawo koma sinthani nkhaniyo!

Kodi ndi Chikondi Chenicheni Kapena Kungotengeka Maganizo?

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe tanthauzo la kutengeka maganizo ndiponso chikondi chenicheni.

Musamangotengera Zochita za Anzanu

Zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kuti muzisankha nokha zochita mwanzeru.

Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti

Chitani zinthu mosamala mukamacheza ndi anzanu pa Intaneti.

Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti

Chitani zinthu mosamala mukamacheza ndi anzanu pa Intaneti.

Kodi Mnzako Weniweni Ungamudziwe Bwanji?

N’zosavuta kupeza anzanu amene sangakuthandizeni, koma kodi mungapeze bwanji mnzanu weniweni?

Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu amavutitsa anzawo komanso zimene mungachite kuti asiye kukuvutitsani.