Zimene mungachite

Muzisankha anzanu mwanzeru. Kuyankhira nkhani zosayenera zokhudza kugonana zimene anzanu akukambirana kungakuchititseni kuti muziganizira kwambiri zogonana. Ngati anzanu ayamba kukambirana nkhani zoterezi, nthawi zambiri mukhoza kupeza njira yabwino yochokera pamalopo, m’njira yosadzionetsa ngati wolungama kwambiri. Kuchita zimenezi kungachititse kuti anzanuwo asakusekeni.

Kodi mungalolere kuti mavailasi alowe mukompyuta yanu? Choncho musalolere kuti maganizo oipa okhudza chiwerewere alowerere mumtima mwanu.

Pewani zosangalatsa zolimbikitsa chiwerewere. Masiku ano, zosangalatsa zambiri zimachititsa anthu kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi? Limati: “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Choncho, muzipeweratu zosangalatsa zilizonse zimene zingakuchititseni kuti mukhale ndi chilakolako chogonana.

Musaiwale mfundo iyi: Kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana si tchimo. Ndipotu Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi m’njira yakuti azikhala ndi chilakolako chogonana, ndiponso anayambitsa banja n’cholinga choti anthu azitha kukhutiritsa chilakolako chimenechi. Choncho, mukakhala ndi chilakolako chofuna kugonana cha mphamvu kwambiri, musaganize kuti ndinu munthu woipa kwambiri ndipo simungathe kudziletsa.

Dziwani izi: Munthu amasankha yekha zinthu zimene akufuna kuziganizira kwambiri. Choncho mungakwanitse kupewa kuganizira kwambiri zachiwerewere komanso kuchita khalidweli ngati mutafuna kutero.