Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ndingatani Ngati Palibe Munthu Amene Ndingacheze Naye Momasuka?

Kodi Ndingatani Ngati Palibe Munthu Amene Ndingacheze Naye Momasuka?

Zimene mungachite

Choyamba, zindikirani anthu amene mumavutika kwambiri kuti mucheze nawo momasuka.

Zaka zawo:

Sindicheza momasuka ndi . . .

 • achinyamata ofanana nawo zaka

 • achinyamata aakulu kuposa ineyo

 • anthu akuluakulu

Zochita zawo:

Sindicheza momasuka ndi . . .

 • akatswiri amasewera

 • anthu a luso linalake

 • anthu ophunzira kwambiri

Umunthu wawo:

Sindicheza momasuka ndi anthu . . .

 • osadzikayikira

 • otchuka

 • a m’gulu limodzi amene amangocheza okhaokha

Chachiwiri, pamawu otsatirawa, sankhani zimene mumachita mukakhala ndi anthu amene tawatchula pamwambawa.

 • Ndimanamizira kuti zokonda ndi zochita zanga n’zofanana ndi zawo.

 • Ndimangonyalanyaza zimene akunena n’kuyamba kuwauza zinthu zimene ineyo zimandisangalatsa.

 • Ndimangokhala phee, osalankhula, ndipo mpata ukapezeka, ndimachoka nthawi yomweyo.

Chachitatu, muziyamba ndinuyo kukhala womasuka. Nthawi zonse musamangodikira kuti anthu ena ayambe kucheza nanu. Nthawi zina inuyo muzikhala woyamba kucheza ndi ena. (Afilipi 2:4) Kodi mungatani kuti mukwanitse kuchita zimenezi?

Musamangoganiza zocheza ndi anthu a msinkhu wanu okhaokha. Taganizirani izi: Kodi n’zomveka kumadandaula kuti mukusowa anthu ocheza nawo pamene mumangofuna kucheza ndi anthu a msinkhu wanu basi? Kuchita zimenezi kuli ngati kufa ndi ludzu mwendo uli m’madzi.

Mayi anga ankandilimbikitsa kuti ndizicheza ndi anthu akuluakulu. Iwo ankandiuza kuti ndidzadabwa kuona kuti ndikugwirizana nawo pa zinthu zambiri. Mayi ankanenadi zoona chifukwa malangizo awo andithandiza kuti ndikhale ndi anzanga ambiri.”—Anatero Helena, wazaka 20.

Phunzirani kucheza ndi anthu. Chinsinsi chake chagona pa (1) kumvetsera, (2) kufunsa mafunso ndi (3) kusonyeza chidwi chenicheni pa zimene akunena.—Yakobo 1:19.

Ndimayesetsa kumvetsera anthu ena akamalankhula m’malo moti ineyo ndizingolankhula. Ndipo ikafika nthawi yoti ndilankhule, ndimayesetsa kuti ndisamangonena za ineyo kapena zinthu zimene munthu winayo sangasangalale nazo.”—Anatero Serena, wazaka 18.

Munthu wina akayamba kunena zinthu zimene sindikuzidziwa bwino, ndimamupempha kuti andifotokozere momveka, ndipo nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti andiuze zambiri.”—Anatero Jared, wazaka 21.

Ndine munthu wamanyazi, choncho ndimachita kudzikakamiza kuti ndizicheza ndi anthu. Komabe ndinaona kuti munthu amafunika kukhala womasuka kuti akhale ndi anzake. Chotero, ndaphunzira kukhala womasuka, ndipo ndimacheza ndi anthu.”—Anatero Leah, wazaka 16.