Baibulo limati: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Koma zimaoneka kuti achinyamata ambiri omwe amafuna kuchita masewera olimbitsa thupi, saikirapo mtima pa masewerawo.

  • “Simungakhulupirire kuti ana ambirimbiri analephera phunziro la masewera olimbitsa thupi kusekondale. Komatu phunziro limeneli ndi mpunga weniweni.”—Richard, wazaka 21.

  • “Ena amaganiza kuti, ‘Palibe chifukwa chomadzivutitsira n’kutuluka m’nyumba n’kumapsa ndi dzuwa pochita masewera olimbitsa thupi mpaka thukuta kamukamu. Bola kungokhala pampando n’kumachita masewera a pakompyuta kapena pa TV.’”—Ruth, wazaka 22.

Ngati inunso mukuona choncho, taonani ubwino wokhala ndi ndandanda yabwino yochitira masewera olimbitsa thupi.

Ubwino woyamba: Amathandiza kuti musamadwaledwale. Bambo anga ankakonda kundiuza kuti, ‘Ngati sukupeza nthawi yochita masewera olimbitsa thupi ndiye kuti ukufufuza nthawi yodwala.’”—Anatero Rachel wazaka 19.

Ubwino wachiwiri: Amathandiza kuti muziganiza bwino. Mtsikana wina wazaka 16 dzina lake Emily anati: “Ndikakhala ndi zambiri m’mutumu, kuthamanga kumandithandiza kuti ndiyambenso kuganiza bwino. Ndikathamanga ndimamva bwino thupi lonse ndiponso maganizo anga amakhala m’malo.”

Ubwino wachitatu: Amathandiza kuti muzisangalala. Ndimasangalala kuyendayenda panja osati kungokhala m’nyumba. Choncho ndimakonda kuchita masewera monga kukwera phiri, kusambira ndiponso kukwera njinga.” Anatero Ruth.

Mfundo Yothandiza: Muziyesetsa kuchita masewera olimbitsa thupi kwa mphindi zosachepera 20 katatu pa mlungu. Muzisankha kuchita masewera omwe mumawakonda ndipo muziwachita mwakathithi.

Kumbukirani izi: N’zoona kuti nthawi zina munthu amatha kukhala wathanzi mwachibadwa. Koma nthawi zambiri munthu amakhala wathanzi kapena ayi chifukwa cha zimene munthuyo amasankha kuchita pamoyo wake. Choncho mukaona kuti mukufunikira kuchita masewera olimbitsa thupi, inuyo ndi amene mungasankhe kuchita masewerawo.