Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigona Mokwanira?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigona Mokwanira?

Baibulo limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Kusagona mokwanira kumalepheretsa munthu kuganiza bwino komanso kuchita zinthu moyenera.

  • “Ndikapanda kugona mokwanira, mutu wanga suyenda bwino. Ndimalephera kuganiza bwinobwino.”—Rachel, wazaka 19.

  • “Cha m’ma 2 koloko masana, ndimatopa koopsa moti ndimayamba kusinza ngakhale ndikucheza ndi anzanga.”—Kristine, wazaka 19.

Kodi inuyo simugona mokwanira? Ngati zili choncho, taonani zimene anzanu ena achita kuti athane ndi vutoli.

Muzipewa kugona mochedwa. Ndakhala ndikuyesetsa kwambiri kuti ndisamagone mochedwa,” anatero Catherine wazaka 18.

Musamakomedwe n’kucheza. Nthawi zina anzanga amandiimbira foni kapena kunditumizira mameseji usiku kwambiri. Koma tsopano ndaphunzira kusiya kucheza n’kupita kukagona.”—Anatero Richard, wazaka 21.

Mukhale ndi nthawi yodziwika bwino imene muzigona komanso kudzuka. Jennifer wazaka 20 anati: “Masiku ano ndikuyesetsa kugona pa nthawi yofanana komanso ndili ndi nthawi yodziwika bwino yodzukira tsiku lililonse.

Mfundo Yothandiza: Tsiku lililonse, muziyesetsa kugona kwa maola osachepera 8.

Kugona mokwanira kumathandiza kwambiri. Mwachitsanzo, thanzi lanu limakhala labwino, ndipo thanzi labwino limakuthandizani kuti muzioneka bwino, muzisangalala komanso muziganiza ndi kuchita bwino zinthu.

Mosiyana ndi zinthu zina pa moyo zomwe simungathe kuzisintha, n’zotheka kusintha zina n’zina zokhudza thanzi lanu. Pa nkhaniyi, mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Erin anati: “Kuti munthu akhale ndi thanzi labwino, zimadalira pa zimene munthuyo akuchita.