Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tisamachite zinthu mopitirira malire.’ (1 Timoteyo 3:⁠2) Zimenezi zikukhudzanso mmene mumadyera. Choncho, mungachite bwino kutsatira mfundo zotsatirazi.

Musamakhute kwambiri. Mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Julia anati: “Poyamba ndinkadya pang’ono kwambiri kuti ndisanenepe. Koma masiku ano, ndimasiya kudya ndikangoona kuti ndakhuta.

Musamakonde kudya zakudya zonenepetsa. Peter, mnyamata wazaka 21 anati: “M’mwezi umodzi wokha, ndinachepetsa kulemera kwanga ndi makilogalamu 5 chifukwa ndinasiya kumwa zakumwa zoziziritsa kukhosi zotsekemera kwambiri.

Musamadye pafupipafupi. Erin, yemwe ndi mtsikana wazaka 18, anati: “Ndimapewa kudya pafupipafupi.

Mfundo Yothandiza: Musamaphonye kudya chakudya cha m’mawa, masana kapena chamadzulo. Ngati mungamaphonye chakudya, ndiye kuti muzimva njala kwambiri moti pa nthawi imene mukufuna kudya, mungadye mopitirira malire.

N’zoona kuti nthawi zina anthu ena omwe alibe vuto lonenepa, amatha kuona ngati saoneka bwino n’kumafuna kuti nawonso achepetse thupi lawo. Komabe, ngati inuyo muli ndi vuto lonenepa ndipo mukufuna kuchepetsa thupi lanu, taonani zimene zinathandiza mtsikana wina dzina lake Catherine, yemwe analinso ndi vuto lonenepa.

“Ndinali wonenepa kwambiri ndipo sindinkasangalala ndi mmene ndinkaonekera.

“Ndinayeserapo mobwerezabwereza kuti ndichepetse thupi langa ndipo ndinkadya zakudya zapadera, koma sizinathandize. Nditafika zaka 15, ndinatsimikiza kuti zivute zitani, ndiyenera kuchepetsa thupi langa basi. Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndiyenera kupeza njira yabwino yochepetsera thupi langa kuti ndisadzanenepenso kwa moyo wanga wonse.

“Ndinagula buku lofotokoza mitundu ya zakudya zoyenerera komanso masewera olimbitsa thupi oyenerera, kenako ndinayamba kutsatira zimene ndinawerengazo. Ndinatsimikiza kuti ndisasiye kutsatira malangizowo ngakhale zinthu zivute chotani.

“Zimenezi zinandithandiza kwambiri. M’chaka chimodzi chokha, ndinachepetsa thupi langa ndi makilogalamu 27. Kwa zaka ziwiri tsopano, ndayesetsa kuti ndisanenepenso. Komatu poyamba ndinkaona ngati zimenezi sizingachitike.

“Ndikuona kuti zinthu zandiyendera osati chifukwa ndinayamba kusamala pa nkhani ya zakudya basi, koma ndinasintha mmene ndimachitira zinthu pa moyo wanga.”​​—⁠Anatero Catherine, wazaka 18.