ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhala Wokhumudwa?
“Munthu aliyense akakhumudwa, ndimayesetsa kum’thandiza kuti ayambenso kusangalala. Koma kenako ndimapita kunyumba n’kukadzitsekera m’chipinda mwanga n’kuyamba kulira, ndipo anthu ambiri sadziwa kuti ndimachita zimenezi.”—Anatero Kellie.
“Ndikakhumudwa ndimakonda kukhala pandekha. Anthu ena akandiitana kuti tipite kwinakwake, ndimayesetsa kupeza chifukwa chokanira. Komanso ndimaonetsetsa kuti anthu a m’banja mwathu asadziwe kuti ndakhumudwa. Iwo amangoganiza kuti ndili bwinobwino.”—Anatero Rick.
Kodi munayamba mwakhalapo ndi maganizo ofanana ndi a Kellie kapena Rick? Ngati ndi choncho, musafulumire kuganiza kuti muli ndi vuto. Zoona zake n’zakuti aliyense amakhumudwa nthawi zina. Ngakhale amuna ndi akazi ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankakhumudwa.—1 Samueli 1:6-8; Salimo 35:14.
Nthawi zina mungadziwe chimene chakuchititsani kuti mukhumudwe, koma nthawi zina simungadziwe. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Anna, anati: “Nthawi zina zinthu zimene zimakukhumudwitsa zimakhala zazing’ono. Munthu akhoza kukhumudwa nthawi ina iliyonse ngakhale pamene alibe mavuto alionse. N’zovuta kumvetsa koma zimachitika.”
Kaya mukudziwa chimene chayambitsa kuti mukhumudwe kapena ayi, kodi mungatani ngati mumangokhala wokhumudwa? Tayeserani kutsatira malangizo otsatirawa:
Uzani munthu wina. Pamene Yobu anali m’mavuto adzaoneni, ananena kuti: “Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.”—Yobu 10:1.
Kellie: Ndikauza munthu wina vuto langa, ndimapepukidwa kwambiri chifukwa ndimaona kuti tsopano winawake akumvetsa zimene zikundichitikira. Ndimaona ngati ndinali m’dzenje lakuya ndipo wina wandiponyera chingwe n’kunditulutsamo.
Lembani mmene mukumvera. Ngati nthawi zambiri mumakhala wokhumudwa, mwina mungachite bwino kulemba mmene mukumvera. Davide anauzidwa ndi Mulungu kulemba m’masalimo mfundo ina yosonyeza kuti nthawi zina Davideyo ankakhumudwa kwambiri. (Salimo 6:6) Kulemba zimenezi kungakuthandizeni ‘kusunga nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.’—Miyambo 3:21.
Heather: Kulemba mmene ndikumvera kumandithandiza kuti ndimvetse bwinobwino zimene zikundichitikira. Ukalemba mmene ukumvera n’kudziwa zimene zikuchititsa kuti udzimva choncho, umapepukidwa.
Muzipemphera. Baibulo limanena kuti mukauza Mulungu nkhawa zanu, “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.
Esther: Ndinkayesetsa kufufuza zinthu zimene zinkachititsa kuti ndizikhumudwa, koma sindinapeze chilichonse. Kenako ndinapempha Yehova kuti andithandize kukhala wosangalala chifukwa ndinali nditatopa n’kumangokhala wokhumudwa popanda chifukwa chilichonse. Pemphero linandithandiza kwambiri. Musamanyalanyaze kupemphera chifukwa pemphero ndi lamphamvu.
Munthu amene amangokhala wokhumudwa amakhala ngati ali m’dzenje lakuya. Koma atachita khama komanso anthu ena atamuthandiza, angatulukemo
Yesani izi: Gwiritsani ntchito Salimo 139:23, 24 monga chitsanzo cha mmene mungapempherere kwa Yehova. Muuzeni zakukhosi kwanu ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni kudziwa zimene zimachititsa kuti muzikhumudwa.
Kuwonjezera pa mfundo zimene zatchulidwazi, mukhozanso kupeza mfundo zina zothandiza m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Kuwerenga nkhani zolimbikitsa zopezeka m’Baibulo kungakuthandizeni kuti muziganizira zinthu zolimbikitsa, muzikhala wosangalala komanso kuti muzichita zinthu zabwino.—Salimo 1:1-3.
Ngati mukupitirizabe kukhala wokhumudwa
Ryan anati: “Nthawi zina kukacha m’mawa sindifuna kudzuka chifukwa ndimaopa kuti ndingakumane ndi zinthu zinanso zokhumudwitsa.” Ryan amadwala matenda ovutika maganizo. Pali achinyamata ambiri amene amadwalanso matendawa ndipo kafukufuku wasonyeza kuti wachinyamata mmodzi pa achinyamata 4 alionse amadwala matenda ovutika maganizo pa nthawi inayake pa moyo wake.
Kodi mungadziwe bwanji ngati mukudwala matenda ovutika maganizo? Zizindikiro zina ndi monga izi: Kusinthasintha, pena kukhala wosangalala kwambiri ndipo penanso wokhumudwa kwambiri; kusafuna kucheza ndi anthu; kusafuna kuchita chinthu chilichonse; kusintha kadyedwe ndi kagonedwe; kumangoganizira kuti ndiwe munthu wosafunika kapena kumangodziimba mlandu pa zinthu zoti sunalakwe.
N’zoona kuti pafupifupi aliyense nthawi zina amatha kusonyeza chizindikiro chimodzi kapena zingapo mwa zizindikiro zimenezi. Komabe ngati mupitirizabe kusonyeza zizindikiro zimenezi kwa milungu ingapo, mungachite bwino kupempha makolo anu kuti mukaonane ndi dokotala. Dokotala angakuthandizeni kudziwa ngati mukudwala matenda ovutika maganizo, kapena ayi.
Ngati mukudwala matenda ovutika maganizo, palibe chifukwa chochitira manyazi. Anthu ambiri akapatsidwa mankhwala kuchipatala amayamba kupeza bwino, mwina kuposa mmene akhala akumvera m’mbuyo monsemu. Choncho, kaya mumakhala wokhumudwa chifukwa chakuti muli ndi matenda ovutika maganizo kapena pa zifukwa zina, muziganizira mawu otonthoza amene amapezeka pa Salimo 34:18. Lembali limati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”