ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndafika Poti N’kulowa M’banja?
Musanayankhe funsoli, muyenera kudzidziwa bwino. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo zotsatirazi:
Mmene mumachitira zinthu ndi abale anu
Kodi mumachita bwanji zinthu ndi makolo komanso abale anu? Kodi nthawi zambiri mumawapsera mtima, mwina mpaka kufika powalankhula mawu achipongwe? Kodi iwowo anganene chiyani za inuyo pa nkhaniyi? Mmene mumachitira zinthu ndi achibale anu zimasonyeza mmene muzidzachitira zinthu ndi mkazi kapena mwamuna wanu.—Aefeso 4:31.
Mtima umene mumasonyeza
Zinthu zikavuta, kodi mumataya mtima msanga? Kodi ndinu wololera, kapena mumamva zanu zokha? Kodi mumatha kuchita zinthu modekha mukapanikizika? Kodi ndinu woleza mtima? Panopa mukamayesetsa kukhala ndi makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa, zidzakuthandizani kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino m’tsogolo.—Agalatiya 5:22, 23.
Ndalama
Kodi mumatha kugwiritsa ntchito bwino ndalama? Kodi nthawi zambiri mumakhala ndi ngongole? Kodi mungathe kukhalitsa pa ntchito? Ngati simungathe, n’chifukwa chiyani? Kodi n’chifukwa cha ntchitoyo kapena bwana wanu? Kapena n’chifukwa cha khalidwe linalake loipa limene muyenera kusintha? Ngati simutha kugwiritsa ntchito bwino ndalama pamene muli nokha, kodi mungadzakwanitse bwanji kugwiritsa ntchito bwino ndalama m’banja lanu?—1 Timoteyo 5:8.
Ubwenzi wanu ndi Mulungu
Ngati ndinu wa Mboni za Yehova, kodi mukuchita zotani kuti mupitirize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu? Kodi mumayesetsa panokha kuwerenga Mawu a Mulungu, kupita mu utumiki ndiponso kuyankha kapena kuchita nawo zinthu zina pamisonkhano yachikhristu? M’pofunika kuti mukhale pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Mulungu, chifukwa munthu yemwe mungadzamange naye banja adzafunika munthu woteroyo.—Mlaliki 4:9, 10.
Mukadzidziwa bwino nokha ndiye kuti mudzathanso kupeza munthu woyenerera amene angakuthandizeni osati kukufooketsani. Mudzatha kupeza munthu yemwe angakulimbikitseni kuti mupitirize kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kuti ubwenzi wanu ndi Mulungu upitirize kukhala wolimba.