Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingatani Ngati Anzanga Akundikakamiza Kuti Ndizichita Zoipa?

Kodi Ndingatani Ngati Anzanga Akundikakamiza Kuti Ndizichita Zoipa?

Zimene Mungachite

Choyamba, zindikirani kuti vuto lililonse limene lingabwere chifukwa cha zochita zanu lidzakhudza inuyo. Izi zingakhale choncho ngakhale kuti anzanu ndi omwe anakukakamizani kuchita zomwe zakubweretserani mavutozo.

Chachiwiri, zindikirani chinthu choipa chimene anzanuwo amakukakamizani kwambiri kuti muchite.

Kenako, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi malo ndiponso nthawi iti imene anzanga angandikakamize kwambiri kuti ndichite zoipazi?’ (Kodi ndi kusukulu? Kuntchito? Kapena kumalo ena?) Kuzindikira nthawi ndi malo amene mungakakamizidwe kuti muchite zoipa kungakuthandizeni kuti mupewe mayesero amenewa.

Tsopano, mukazindikira zimenezi ndiye kuti mwakonzeka kulimbana ndi vutoli. Chinthu choyamba chimene mungachite n’kudziwa zochita kuti mupewe kukumana ndi anzanu amene amakukakamizani kuchita zoipawo. (Chitsanzo: Ngati nthawi zonse pochokera kusukulu mumakumana ndi anzanu a m’kalasi amene amakukakamizani kuti musute fodya, mungachite bwino kusintha njira kuti musamakumane nawo.) Muzikumbukira mfundo iyi: Anthu amene amati ndi anzanu, koma amakukakamizani kuchita zinthu zoipa, ndiye kuti si anzanu enieni.

Mukagonja pa mayesero, mumakhala kapolo wa zilakolako zanu

N’zoona kuti sikuti mungapeweretu kukumana ndi anthu onse amene angakukakamizeni kuchita zoipa. Nthawi ina iliyonse, mwina anthu ena amene simukuwayembekezera, angakukakamizeni kapena kukunyengererani kwambiri kuti muchite zoipa. Kodi mungatani zoterezi zikachitika?

Nthawi zonse muzikhala okonzeka

Taganizirani izi: Yesu ankadziwa bwino zimene angachite pa nkhani ya makhalidwe abwino. Iye anatsimikiza ndi mtima wonse kuti nthawi zonse adzamvera Atate wake. (Yohane 8:28, 29) Choncho, chinthu chofunika kwambiri n’kudziwiratu chochita pa nkhani inayake.

Tayesani izi. Yesani kuganizira zifukwa ziwiri zimene zingakuchititseni kupewa kuchita zinthu zoipa zimene anzanu amakukakamizani nthawi zambiri kuti muchite. Kenako ganizirani zinthu ziwiri zimene mungachite zomwe zingakuthandizeni kuti muthane ndi vutolo.

Musalole ngakhale pang’ono kuti anzanu azikusankhirani zochita. Muzisonyeza kuti ndinu wokhwima maganizo posankha nokha kuchita zinthu zomwe zili zoyenera. (Akolose 3:5) Nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kulimbana ndi mayesero oterewa.—Mateyu 6:13.