Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ndingati Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?

Kodi Ndingati Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?

Zimene mungachite

Ganizirani izi: Kodi khalidwe lanu komanso zinthu zambiri zimene mumachita zimachititsa kuti makolo anu asamakukhulupirireni?

Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimawauza zoona zokhazokha makolo anga pa nkhani ya kumene ndikupita ndi zimene ndikuchita?’

Taonani zimene achinyamata anzanu ankachita.

 Lori  Beverly

 Lori

Ndinkalemberana maimelo mwachinsinsi ndi kamnyamata kenakake. Makolo anga atadziwa, anandiuza kuti ndisiyiretu zimenezi. Ndinawalonjeza kuti ndisiya, koma ndinapitiriza kuchita zimenezi kwa chaka chathunthu. Ndinkalembabe maimelowo ndipo makolo anga akandipezerera ndinkapepesa n’kulonjeza kuti sindidzabwerezanso, koma kenaka ndinkamulemberanso. Zimenezi zinapangitsa kuti makolo anga asiyiretu kundikhulupirira.

Kodi mukuganiza kuti makolo a Lori anasiyiranji kumukhulupirira?

Zikanakhala kuti inuyo ndinu makolo a Lori, kodi mukanachita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani mukanachita zimenezo?

Kodi Lori anayenera kuchita chiyani pofuna kusonyeza kuti ndi wokhwima maganizo makolo ake atamuletsa koyamba kulemba maimelo?

 Beverly

Makolo anga sankandikhulupirira pa nkhani ya kucheza ndi anyamata, koma panopo ndinadziwa chifukwa chake. N’chifukwa choti ndinkazolowerana kwambiri ndi anyamata angapo amene anali aakulu kwa ineyo ndi zaka ziwiri. Komanso ndinkatha nthawi yaitali ndikulankhula nawo pa foni, ndipo tikakhala pagulu, nthawi yaitali ndinkangocheza ndi iwowo basi. Motero makolo anga anandilanda foni kwa mwezi wathunthu, ndipo anayamba kundiletsa kupita kulikonse kumene kunali anyamatawo.

Zikanakhala kuti inuyo ndinu makolo a Beverly, kodi mukanachita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani mukanachita zimenezo?

Kodi mukuganiza kuti makolo a Beverly anali okhwimitsa zinthu kwambiri? N’chifukwa chiyani mukuganiza choncho?

Kodi Beverly akanatani kuti makolo ake ayambenso kumukhulupirira?

Kodi Mungatani Kuti Ayambenso Kukukhulupirirani?

Zimene mungachite

Kuchoka paunyamata kufika pa kukhala munthu wamkulu wodalirika kuli ngati kukwera masitepe kuchoka pansi kupita pamwamba

Choyamba, dziwani chimene chinachititsa kuti makolo anu asamakukhulupirireni.

 • Kufika panyumba nthawi yabwino

 • Kuchita zimene ndalonjeza

 • Kusunga nthawi

 • Kusamala ndalama

 • Kumaliza ntchito zapakhomo

 • Kudzuka nthawi yabwino osadikira kudzutsidwa

 • Kusamala kuchipinda kwanga

 • Kunena zoona zokhazokha

 • Kugwiritsa ntchito foni kapena kompyuta mwanzeru

 • Kuvomereza zolakwa ndiponso kupepesa

 • Zina

Chachiwiri, khalani ndi cholinga. Yesetsani kutsatira mfundo zimene mwaona kuti mukufunika kusintha. Tsatirani malangizo a m’Baibulo akuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale.” (Aefeso 4:22) Mukamachita zimenezi, aliyense kuphatikizapo makolo anu, adzaona kuti mukusintha.—1 Timoteyo 4:15.

Chachitatu, auzeni makolo anu zimene mwasankha kusinthazo. M’malo modandaula kuti makolowo akufunika kumakukhulupirirani kwambiri, afunseni mwaulemu zimene mungachite kuti ayambirenso kukukhulupirirani.

Chenjezo: Musayembekezere kuti makolo anu angayambe kukukhulupirirani nthawi yomweyo. N’zosakayikitsa kuti angayembekeze kaye kuti aone ngati mwatsimikizadi kuchita zimene mwalonjeza. Zikatere yesetsani kuchita zinthu mokhulupirika. M’kupita kwa nthawi, makolo anu angayambe kukukhulupirirani kwambiri. Izi n’zimene zinachitikira Beverly uja. “Zimavuta kuti anthu ayambenso kukukhulupirira koma sizivuta kuti asiye kukukhulupirira. Panopo makolo anga anayambanso kundikhulupirira ndipo ndimasangalala nazo kwabasi.”

Dziwani izi: Mukamachita zinthu zosonyeza kuti ndinu munthu wokhulupirika kwambiri, anthu adzayambanso kukukhulupirirani kwambiri.