Mwina mukudziwa achinyamata ena amene amapita kwawo nthawi iliyonse imene afuna, amavala mmene akufunira, komanso amatha kupita kocheza nthawi iliyonse ndiponso malo alionse amene akufuna. N’kutheka kuti makolo awo amangotanganidwa ndi ntchito moti sazindikira zimene ana awo amachita.

Komatu Baibulo limasonyeza kuti kulera ana mwanjira imeneyi sikuthandiza. (Miyambo 29:15) M’dzikoli anthu amachita zinthu mopanda chikondi chifukwa chakuti amangoganizira zawo zokha ndipo anthu ambiri amene amachita zimenezi amakhala kuti anakulira m’banja limene makolo awo sanawaikire malamulo.​—2 Timoteyo 3:​1-5.

Muziona kuti malamulo amene makolo anu anakuikirani ndi umboni wakuti amakukondani ndipo musamasirire achinyamata amene makolo awo amawalola kuchita chilichonse chimene afuna. Makolo akamaikira ana awo malamulo oyenerera, amakhala akutsatira Yehova Mulungu amene anauza anthu ake kuti:

“Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.”​—Salimo 32:8.