Onani zimene mungachite kuti zinthu zisafike poipa kwambiri mukalakwitsa.

Muzinena zoona. Mukamanama pamene mwaphwanya lamulo, makolo anu angasiyiretu kukudalirani. Choncho muzilankhula moona mtima zimene zachitika.​​—⁠Miyambo 28:⁠13.

  • Musamapereke zifukwa zosonyeza kuti palibe cholakwika ndi zimene mwachitazo.

  • Nthawi zonse muzikumbukira kuti “kuyankha modekha kumabweza mkwiyo.”​—⁠Miyambo 15:⁠1.

Muzipepesa. Mukasonyeza kuti mwakhudzidwa ndi zinthu zimene mwalakwitsa, makolo anu angakuchepetsereni chilango chimene mukufunika kulandira. Komabe mukufunika kupewa kupepesa mwachinyengo.

Muzivomereza chilango. Kuvomereza zotsatirapo za zochita zanu kumasonyeza kuti ndinu munthu wanzeru. Mukalakwa muyenera kuchita zonse zimene mungathe kuti makolo anu ayambirenso kukudalirani.​—⁠Miyambo 20:⁠11.

Muzikumbukira kuti makolo anu ali ndi udindo wokupatsani malamulo oyenera. Ndipotu Baibulo limanena kuti muzimvera ‘lamulo la bambo anu ndipo musasiye malangizo a mayi anu.’​—⁠Miyambo 6:⁠20.

Ngati mukufuna kuti makolo anu azikupatsani ufulu wambiri

  • Muzimvera malamulo amene anakupatsani.

  • Muziyesetsa kuti mukhale mwana wabwino.