Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingatani Ngati Ndilibe Mnzanga?

Kodi Ndingatani Ngati Ndilibe Mnzanga?

Zimene mungachite

 1. Muziganizira kwambiri zimene mumachita bwino. (2 Akorinto 11:6) Ngakhale kuti ndibwino kuzindikira kuti pali zinthu zina zomwe simuchita bwino kwenikweni, muzikumbukiranso kuti pali zambiri zimene mumachita bwino. Mukazindikira zimenezi simudzavutika kuthana ndi maganizo odzikayikira, omwe nthawi zambiri amachititsa munthu kuti aziopa kucheza ndi ena. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimachita bwino kwambiri pa zinthu ziti?’ Ganizirani za luso losiyanasiyana kapena makhalidwe enaake amene muli nawo.

 2. Muzichita chidwi ndi ena. Poyambirira, mukhoza kusankha anthu angapo amene mukufuna kuwadziwa bwino. Pa mfundo imeneyi, mnyamata wina dzina lake Jorge anati: “Kupatsa munthu moni komanso kumufunsa zina ndi zina zokhudza ntchito imene akugwira kumandithandiza kuti ndidziwane bwino ndi munthuyo.”

Mungaike mlatho pa zinthu zimene zimakusiyanitsani ndi anzanu

 Yesani izi: Musamangocheza ndi anthu a msinkhu wanu okhaokha. M’Baibulo muli zitsanzo za anthu osiyana kwambiri msinkhu koma anali pa ubwenzi wabwino. Ena mwa anthu amenewa anali Rute ndi Naomi, Davide ndi Yonatani komanso Timoteyo ndi Paulo. (Rute 1:16, 17; 1 Samueli 18:1; 1 Akorinto 4:17) Muzikumbukiranso kuti kucheza bwino ndi ena kumafuna kumvetserana, osati munthu m’modzi kumangolankhula yekhayekha. Anthu amasangalala ndi munthu yemwe amamvetsera iwo akamalankhula. Choncho manyazi asakulepheretseni kucheza ndi ena chifukwa sikuti mumayenera kumangolankhula nokhayi

 3. Yesetsani kukhala wokoma mtima. (1 Petulo 3:8) Ngakhale mutakhala kuti simukugwirizana ndi zimene wina akunena, muzimvetserabe modekha ndipo musamamudule. Muzingoona mfundo zimene mukugwirizana nazo. Koma ngati mukuona kuti mukufunika kunena maganizo anu pa mfundo yomwe simukugwirizana nayo, chitani zimenezo modekha komanso mwanzeru.

 Yesani izi: Muzilankhula ndi ena m’njira imene mukufuna kuti ena azikulankhulani. Koma mukamalankhula monyoza ena kapena mosonyeza kuti ndinu munthu wabwino kuposa iwowo, zimachititsa kuti anthu enawo azikupewani. Koma iwo angakukondeni kwambiri ngati ‘nthawi zonse mawu anu amakhala achisomo.’—Akolose 4:6.