Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhoza Bwino Kusukulu?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhoza Bwino Kusukulu?

Zimene mungachite

Musamadzikayikire. Musamaganize kuti ndinu wolephera basi ndipo simungasinthe. Mukayamba kuganiza zoti mulibe nzeru ndipo simungachite bwino zinthu zinazake, muzichotsa maganizo amenewo n’kuyamba kuganizira zinthu zomwe mumachita bwino. Mwachitsanzo, pamene anthu anayamba kunyoza mtumwi Paulo kuti satha kulankhula bwino, (ngakhale kuti anthuwo mwina sankanena zoona) iye anayankha kuti: “Ngati ndilibe luso la kulankhula, si kuti ndine wosadziwanso zinthu.” (2 Akorinto 10:10; 11:6) Paulo ankadziwa kuti pali zinthu zina zomwe zimamuvuta. Koma ankadziwanso kuti pali zinthu zina zomwe amachita bwino kwambiri. Nanga bwanji inuyo? Kodi ndi zinthu ziti zomwe mumachita bwino? Ngati simukudziwa, bwanji osapempha munthu wina wamkulu yemwe amakudziwani bwino kuti akuuzeni zinthu zomwe mumachita bwinozo? Munthuyo angakuthandizeni kudziwa zinthuzo komanso angakuuzeni zimene mungachite kuti muzichita zinthuzo mwaluso kwambiri.

Yesetsani kukhala ndi mtima wokonda kuwerenga. Kuwerenga ndi njira yokhayo imene mungatsatire kuti muzikhoza bwino kusukulu. N’zoona kuti anthu ena akangomva mawu akuti kuwerenga, sasangalala. Komabe kuti zinthu zizikuyenderani bwino, mumafunika kumawerenga. Ndipo mukamayesetsa kuchita khama, mudzayamba kukonda kuwerenga. Komabe kuti mukhale ndi mtima wokonda kuwerenga, pamafunika kugawa bwino nthawi. Monga mwana wasukulu, muzikumbukira kuti kuwerenga kufunikira kukhala chinthu choyamba pamoyo wanu. N’zoona kuti Baibulo limati pali “nthawi yoseka” ndiponso “nthawi yodumphadumpha.” (Mlaliki 3:1, 4; 11:9) Choncho, mofanana ndi achinyamata anzanu, mwina mumafuna kukhala ndi nthawi yosangalala. Koma lemba la Mlaliki 11:4 limatichenjeza kuti: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.” Kodi tikuphunzira chiyani palembali? Musamachite zinthu mozengereza chifukwa palibe chinthu chaphindu chomwe mungachite. Nthawi zonse, kuwerenga kuzikhala patsogolo, masewera pambuyo. Mungakwanitse kuchita zimenezi ngati mutagawa bwino nthawi yanu.

Mofanana ndi mmene kunyamula weti kungalimbitsire thupi lanu, mtima wokonda kuwerenga ungakuthandizeni kuti muzikhoza bwino kusukulu.