Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndikambirane ndi Makolo Anga pa Nkhani ya Malamulo Amene Anandiikira?

Kodi Ndingatani Kuti Ndikambirane ndi Makolo Anga pa Nkhani ya Malamulo Amene Anandiikira?

Zimene mukufunika: Kudziwa zoyenera kunena, mmene mungazilankhulire komanso nthawi yabwino yozilankhulira

Zimenezi ndi zofunika kwambiri chifukwa

  • zimathandiza kuti anthu akumvetseni.

  • zimakuthandizani kuti mumvetse chifukwa chake akukukanizani zimene mukufuna.

Ndipotu ngati mukufuna kuti makolo anu azikuchitirani zinthu monga munthu wamkulu, mufunika kudziwa njira zabwino zolankhulira. Kodi mungatani kuti zimenezi zitheke?

Phunzirani kudziletsa. Munthu amafunika kukhala wodziletsa kuti azilankhulana bwino ndi anthu. Baibulo limanena kuti: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.”Miyambo 29:11.

Apa mfundo ndi yakuti muzipewa kulankhula mopsa mtima, kumenyetsa zitseko, muzipewanso kunyinyirika, ngakhalenso kuyenda mopsa mtima. Koma ngati mungamasonyeze makhalidwe amenewa, makolo anu angakuwonjezereni malamulo m’malo mokuchepetserani.

Yesetsani kumvetsa zimene makolo anu akukuuzani. Mwachitsanzo: Tiyerekeze kuti makolo anu akukuletsani kupita kwinakwake kukasangalala. M’malo mokakamira kupita, mungawafunse kuti:

“Kodi mungandilole kupita ngati nditakhala limodzi ndi mnzanga uja amachita zinthu mwanzeru komanso modalirika?”

Mwina makolo anu sangalolebe kuti mupite. Koma ngati mutamvetsa chifukwa chake akukukanizani kupita, mukhoza kupeza njira yabwino yowapemphera.

Mukamamvera malamulo a makolo anu mumakhala ngati mukubweza ngongole kubanki. Mukamachita zinthu modalirika, adzayamba kukudalirani kwambiri.

Muzichita zinthu modalirika. Tiyerekezere kuti munthu wina wabwereka ndalama kubanki. Ngati atabweza ngongoleyo mokhulupirika, eni ake a bankiyo akhoza kumamukhulupirira ndipo akhoza kudzamubwereka ndalama zambiri m’tsogolo.

N’chimodzimodzinso ndi inuyo. Tinganene kuti muli ndi ngongole ndi makolo anu yomwe ndi kuwamvera. Ndiye ngati simukuwamvera, musadzadabwe akadzachepetsa kukudalirani, mwinanso kusiyiratu kukudalirani.

Koma ngati mutamachita zinthu modalirika ngakhale pa zinthu zazing’ono, makolo anu angayambe kukudalirani.