Zimene mungachite

Pezani malo abwino owerengera. Akhale malo aphee, opanda zosokoneza. Ngati zili zotheka, mukhale ndi tebulo lowerengera. Komanso musayatse TV.

Nthawi ili ngati hatchi imene ikuthamanga kwambiri. Phunzirani kuigwiritsira ntchito mwanzeru

Muzigawa bwino nthawi yanu. Popeza sukulu ndi yofunika kwambiri pa moyo wanu, kuchita homuweki kuzikhala chinthu choyamba pa zochita zanu.

Musamasinthesinthe. Mukhale ndi nthawi yokhazikika yochitira homuweki, ndipo musamaisinthe.

Muzipanga pulani. Sankhani ntchito ya kusukulu imene mukufuna kuiika pamalo oyamba, pamalo achiwiri, kapenanso achitatu. Lembani ntchitozi komanso kutalika kwa nthawi imene mukufuna muthere pa ntchito iliyonse. Muzichonga ntchito iliyonse papepalalo mukamaliza kuigwira.

Muzipumirako. Mukaona kuti mwayamba kutopa, muzipumirako pang’ono. Koma musamachedwe kuyambiranso homuweki yanuyo.

Musamadzikayikire. Muzikumbukira kuti chifukwa chachikulu chimene chimachititsa kuti ana ena azikhoza bwino kwambiri kusukulu kuposa ena, ndi kulimbikira osati nzeru zokha. (Miyambo 10:4) Chotero inunso mungathe kumakhoza bwino. Mukungofunika kuchita khama ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.